32. As-Sajda
1Alif Lam Mim
2Ichi ndi chivumbulutso cha Buku Lopatulika limene mulibe zokayikitsa ndi chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse
3Kodi kapena iwo amati wapeka yekha? Iyayi, ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wake kuti uchenjeze anthu amene kuyambira kale mchenjezi sanadze kwa iwo, kuti iwo akhoza kutsatira njira yoyenera
4Mulungu ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko Sajda 439 lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero Iye adabuka pa mpando wake wachifumu. Inu mulibe wokuyang’anirani kapena wokuthandizani kupatula Iye yekha. Kodi simungaganize
5Iye amalamulira zinthu kuchokera kumwamba mpaka pa dziko lapansi ndipo zidzakwera kudza kwa Iye m’tsiku limene muyeso wake ungathe kuyerekezedwa ndi zaka chikwi chimodzi mwa chiwerengero chomwe inu mumachidziwa
6Uyundiyewodziwazobisikandizooneka, Mwini mphamvu, ndi Mwini chisoni chosatha
7Amene adalenga chilichonse m’maonekedwe abwino. Ndipo adalenga munthu kuchokera ku dothi
8Ndipo adalenga ana ake kuchokera ku dontho lamadzi onyozeka
9Ndipo iye adamuumba munthu mwaubwino ndipo adamuuzira Mzimu wake. Ndipo Iye adakupatsani inu makutu, maso ndi mitima, inu simuthokoza nthawi zambiri
10Iwo adati, “Chiyani! Pamene ife taikidwa m’manda, kodi tingadzalengedwenso?” Ndithudi iwo adakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo
11Nena “Mngelo wa imfa, amene adasankhidwa kukuyang’anirani inu, adzakupangitsani kuti mufe. Kotero inu mudzabwerera kwa Ambuye wanu.”
12Iwe ukadangodzaona mmene anthu ochimwa adzagwetsera mitu yawo pamaso pa Ambuye wawo nati, “Ambuye wathu! Ife taona ndipo tamva. Tsopano tibwezereni pa dziko lapansi ndipo ife tidzagwira ntchito zachilungamo chifukwa ife, ndithudi, takhulupirira.”
13Ife tikadafuna, ndithudi, tikadatsogolera mzimu uliwonse ku njira yoyenera. Koma kuti mawu ochokera kwa Ine adakwanitsidwa. “Ine ndidzadzadza Gahena ndi majini pamodzi ndi anthu.”
14Lawani chilango tsopano, chifukwa inu mudaiwala za tsikuli. Ndipo nafenso takuiwalani. Kotero inu lawani chilango chosatha chifukwa cha ntchito zanu zoipa
15Ndi okhawo amene amakhulupirira chiphunzitso chathu amene chiphunzitsocho chimati chikaphunzitsidwa, amagwa pansi kupembedza ndipo amayamikandikulemekeza Mulunguwawomodzichepetsa
16Iwo amasiya makama awo ndi cholinga chopempha kwa Ambuye wawo mwamantha ndi mwa chikhulupiriro. Ndipo amapereka zaulere kuchokera ku chuma chimene tidawapatsa
17Tsopano palibe munthu amene amadziwa madalitso amene ali kuwasungira m’nkhokwe ngati malipiro a ntchito zawo zabwino
18Kodi munthu wokhulupirira angafanane ndi munthu woswa malamulo ndi woipa? Iyayi, sangafanane
19Iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzalandira minda ngati malo awo okhala chifukwa cha ntchito zawo zabwino zimene anachita
20Ndipo iwo amene amaswa malamulo, malo awo okhala ndi kumoto ndipo nthawi zonse zimene iwo adzafuna kuchokako, adzabwezedwanso komweko. Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti, “Lawani ululu wa moto umene munkati ndi bodza.”
21Ndipo, ndithudi, Ife tidzawalawitsa, chilango cha m’moyo uno chisanadze, chilango choyamba kuti mwina akhoza kutembenuka
22Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amati akakumbutsidwa chiphunzitso cha Ambuye wake, iye amabwerera m’mbuyo? Ndithudi Ife tidzalanga anthu ochimwa
23Ndipo, ndithudi, Ife tidamupatsa Buku Mose ndipo musakayike za kulandira kwake ndipo tidalipanga ilo kukhala chotsogolera ana a Israyeli
24Ndipo tidasankha pakati pawo, atsogoleri amene amapereka malangizo potsatira malamulo athu, pamene iwo anali kupirira ndi kukhulupirira mu chiphunzitso chathu
25Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku louka kwa akufa pa nkhani zimene anali kutsutsana
26Kodi icho sichiwaphunzitsa phunziro kuti kodi ndi mibadwo ingati imene tidaononga iwo asanadze, m’nyumba zawo zimene amalowa ndi kutulukamo? Ndithudi mu izo muli chiphunzitso. Kodi iwo sangamve
27Kodi iwo saona kuti Ife timagwetsa mvula panthaka youma ndi kumeretsa mbewu zimene iwo ndi ziweto zawo zimadya? Kodi alibe maso oti angaone
28Iwo amafunsa kuti “Kodi chiweruzo chimenechi chidzachitika liti ngati zimene munenazi ndi zoona?”
29Nena, “Pa tsiku lachiweruzo, chikhulupiriro cha iwo amene sakhulupirira sichidzawathandiza ndiponso sadzapeza mpumulo.”
30Kotero asiye okha ndipo dikira ndithudi nawonso ali kudikira
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath