31. Luqman
1Alif Lam Mim
2Awa ndi mawu a m’Buku la nzeru
3Chilangizo ndi chifundo kwa anthu angwiro
4Amene amapemphera nthawi zonse, amene amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo amakhulupirira m’moyo umene uli nkudza
5Amenewa ndiwo amene atsogozedwa bwino ndi Ambuye wawo ndipo ndithudi adzakhala opambana
6Koma pakati pa anthu, alipo ena amene amagula nkhani zopanda pake ndi zopanda tanthauzo ndi cholinga chosocheretsa anthu ku njira ya Mulungu ndi kuipanga iyo kukhala chinthu choseketsa. Awa adzalandira chilango chochititsa manyazi
7Ndipo pamene chivumbulutso chathuchilakatulidwakwaiye, iyeamatembenukamonyada kuoneka ngati kuti sadamve china chilichonse, kapena ngati kuti m’makutu mwake muli phula kotero muuzeni za chilango chowawa
8Akakhala iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito za bwino, ndithudi, adzakhala ku Paradiso
9Kukhalamo mpaka kalekale ndi lonjezo loona la Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu ndipo ndi wanzeru zonse
10Iye adalenga kumwamba popanda nsanamira monga muonera ndipo adalenga mapiri pa dziko lapansi kuti mwina dziko likhoza kuyenda pamodzi ndi inu. Ndipo m’dzikomo adaikamo nyama za mtundu uliwonse. Ndipo ife timatumiza mvula kuchokera ku mtambo ndipo timameretsa mbewu za mitundu yosiyanasiyana
11Ichi ndi chilengedwe cha Mulungu ndipo ndionetseni zimene iwo amene amakhala pafupi naye adalenga. Iyayi, anthu opanda chilungamo ndi olakwa
12Ndithudi Ife tidamupatsa nzeru Luqman ponena kuti, “Thokozani Mulungu. Aliyense amene amathokoza Mulungu, amathokoza chifukwa cha mzimu wake ndipo aliyense amene sathokoza, ndithudi, Mulungu sasowa kanthu ndipo ndi wolemekezeka.”
13Ndi pamene Luqman adamuuza mwana wake adamulangiza kuti, “Mwana wanga usamafanizire Mulungu ndi china chilichonse chifukwa ndi tchimo loopsa.”
14Ndipo Ife timamulamula munthu kuonetsa chifundo kwa makolo ake. Movutika amayi ake adamubereka iye ndipo m’zaka ziwiri adamuyamwitsa. Kotero, thokozani Ine ndiponso thokozani makolo anu chifukwa ndi kwa Ine kumene mudzabwerera
15Koma ngati akuuza kuti uzindifanizira Ine ndi china chake chimene siuchidziwa, usawamvere. Aonetsere chifundo ndipo utsatire zochita za iye amene amalapa kwa Ine ndi kundimvera. Ndipo kwa Ine ndi kumene nonse mudzabwerera ndiponso ndidzakuuzani zonse zimene mudachita
16“oh mwana wanga! Choipa ngakhale chitakhala ngati njere ya mpiru imene idakwiriridwa m’kati mwa mwala kapena kwina kulikonse kumwamba kapena pa dziko lapansi, Mulungu adzachitulutsa. Mulungu ali ndi nzeru ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.”
17“Oh mwana wanga! Limbikira kupemphera, khazikitsa chilungamo ndipo udziletse kuchita zoipa. Khala opirira pa chilichonse chimene chidza pa iwe.” Ndithudi! Awa ndi malamulo ofunika amene adalamula Mulungu ndipo ayenera kutsatidwa
18“Usanyodole anthu kapena kuyenda modzitukumula pa dziko. Mulungu sakonda anthu odzitukumula.”
19“Ndipo uyenera kukhala wofatsa ndipo mawu ako azikhala otsika chifukwa mawu aukali kwambiri ndi kulira kwa bulu.”
20Kodi simuona kuti Mulungu wapanga zinthu zimene zili kumwamba ndiponso zimene zili padziko lapansi kukumverani inu ndipo adakupatsani inu zabwino zooneka ndi zosaoneka ndi maso? Ndipo pakati pa anthu pali iye amene amatsutsa zinthu zokhudza Mulungu ngakhale iye sadziwa china chilichonse, kapena chilangizo kapena Buku lopereka muuni
21Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: Tsatirani zimene Mulungu wavumbulutsa iwo amati, Iyayi. Ife sititsatira china chilichonse koma zokhazo zimene tidapeza makolo athu ali kutsatira. Ngakhale kuti Satana ali kuwaitanira iwo ku chilango cha moto
22Aliyense amene adzipereka kwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, amagwiritsa chotsekulira chimene chiyenera kugwiridwa ndipo kwa Mulungu zinthu zonse zidzabwerera
23Koma ngati wina akana kukhulupirira, usalole kuti kusakhulupirira kwakeko kuti kukumvetse chisoni. Kwa Ife, anthu onse adzabwerera ndipo tidzawauza zoona za ntchito zawo. Mulungu amadziwa bwino zonse zimene zili m’mitima mwa anthu
24Ife timawalekerera pa kanthawi kochepa ndipo pomaliza Ife tidzawakankha kupita ku chilango chowawa
25Ndipo ngati iwe uwafunsa kuti ndani amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndithudi, iwo adzati, “Mulungu.” Nena, “Ulemerero ukhale kwa Mulungu.” Iyayi! Ambiri a iwo sadziwa
26Chilichonse chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi cha Mulungu. Ndithudi Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi woyamikidwa
27Ndipo kukadakhala kuti mtengo uliwonse umene uli pa dziko lapansi udasanduka kukhala cholembera ndipo nyanja kusanduka kukhala inki mothandizidwandi nyanja zina zisanu ndi ziwiri ndithudi, mawu a Mulungu sakadatha. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu ndi waluntha
28Kalengedwe kanu ndi kuukitsidwa kwanu kwa akufa si chinthu chovuta ayi. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wowona
29Kodi inu simuona mmene Mulungu amasandulizira usiku kuti ukhale usana ndi usana kuti ukhale usiku ndipo wapangira dzuwa ndi mwezi kuti zizikumverani inu? Ndiponso kodi simuona kuti chilichonse chimayenda m’njira yake mpaka pa nthawi yokhazikitsidwa ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene inu mumachita
30Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu ndiye choonadi ndipo kuti chimene iwo amapembedza kuonjezera pa Mulungu ndi chinthu wamba chabe. Mulungu ndi wapamwamba ndi wamkulu
31Kodiinusimuonammenezombozimayenderapanyanja mwachisomo cha Mulungu ndi mmene amakuonetserani inu zizindikiro zake? Ndithudi muli chiphunzitso mu zimenezi kwa anthu olimbikira ndiponso kwa oyamika
32Ndipo pamene mafunde okhala ngati mapiri awaphimba, iwo amapempha kwa Mulungu modzichepetsa. Koma Iye akangowafikitsa bwino pa mtunda, ena a iwo amatsatira njira ya pakati ndipo palibe amene amakana chiphunzitso chathu koma yekhayo amene sathokoza ndiponso amene ndi wamwano
33oh anthu inu! opani Ambuye wanu ndipo liopeni tsiku limene kholo silidzathandiza mwana wake kapena mwana kuthandiza kholo lake. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Kotero musalole moyo wa padziko lino lapansi kuti ukunyengeni inu kapena kuti Satana akunyengeni pa nkhani zokhudza Mulungu
34Ndithudi Mulungu ndiye yekha amene amadziwa za kudza kwake kwa tsiku lachiweruzo. Ndiye amene amatsitsa mvula ndiponso amadziwa zimene zili m’mimba mwa akazi. Ndipo palibe amene amadziwa zimene zingamuonekere mawa ndipo palibe amene amadziwa dziko limene adzafere. Ndithudi Mulungu ndi Wodziwa ndi Wozindikira
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath