Chisilamu
kubwerera

30. Malo a Ar-Room

1Alif Lam Mim

2Aroma agonjetsedwa

3M’dziko loyandikana nalo ndipo iwo atagonja, pambuyo pake adzapambana

4M’zaka zowerengeka. Mulungu ndiye Mwini ulamuliro ndipo pa tsiku limeneli onse okhulupirira adzakondwera

5Ndi chithandizo cha Mulungu. Iye amathandiza aliyense amene wamufuna. Iye ndi wamphamvu, ndiponso Mwini chisoni chosatha

6Ili ndi lonjezo la Mulungu. Mulungu saphwanya lonjezo lake ndipo anthu ambiri sadziwa

7Iwo amangodziwa zokhazo zimene amaziona za m’moyo uno koma za m’moyo umene uli nkudza, iwo safuna kumva china chilichonse cha izo

8Kodi iwo saganizira pa okha kuti Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zikhala m’menemo mwachoonadi ndi mwa kanthawi yokhazikitsidwa? Ndipo, ndithudi, anthu ambiri amakana zoti adzakumana ndi Ambuye wawo

9Kodi iwo sadayende pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale? Iwo adali ndi mphamvu zambiri kuposa awa, ndipo adakumba nthaka ndiponso adamanga pa nthakayo nyumba zambiri kuposa zimene awa amanga. Ndipo kudadza kwa iwo Atumwi awo ndi chiphunzitso chomveka ndipo sikudali koyenera kuti Mulungu awachitire zinthu zosalungama koma kuti iwo adalakwira mizimu yawo

10Choipa chidatsata munthu amene anali kuchita zoipa chifukwa iwo adakana chiphunzitso cha Mulungu ndipo anali kuwaseka iwo

11Mulungu ndiye amene amalenga zolengedwa ndipo adzazibwereza ndipo ndi kwa Iye kumene mudzabwerera

12Ndipo pa nthawi imene ola lidzadza, anthu onse ochita zoipa adzakhala ndi nkhawa

13Ndipo iwo sadzakhala ndi ena alionse owathandiza ochokera pakati pa milungu yawo imene anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo iwo adzakhala okana milungu yawo

14Ndipo pa nthawi imene ola lidzadza, pa nthawi imeneyi, iwo adzasiyanitsidwa wina ndi mnzake

15Ndipo onse amene adakhulupirira ndipo adachita ntchito zabwino, iwo adzasangalatsidwa m’munda wa Paradiso

16Iwo amene sadakhulupirire ndipo adakana chiphunzitso chathu ndi kukumana kwa m’moyo umene uli nkudza, awa ndiwo amene adzatengedwa kupita ku chilango

17Kotero lemekezani Mulungu pamene mulowa nthawi ya madzulo ndi pamene mulowa nthawi ya m’mawa

18Inde. Kwa Iye kukhale kuyamikidwa kumwamba ndi padziko lapansi ndiponso pa nthawi yamasana ndi yamadzulo

19Iye ndiye amene amadzutsa anthu kuchokera ku anthu akufa ndipo amadzutsa anthu akufa kuchokera ku anthu amoyo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndipo mmenemo ndi mmene mudzaukitsidwire

20Ndipo chimodzi cha zizindikiro zake ndi chakuti Iye adakulengani inu kuchokera ku fumbi, ndipo inu, ndinudi, anthu amene mudamwazidwa

21Ndipo pakati pa zizindikiro china ndi chakuti Iye adalenga akazi kuchokera mwa inu kuti mukhoza kupeza mpumulo mwa iwo ndipo adaika pakati panu chikondi ndi chisoni. Ndithudi muli phunziro muichi kwa anthu amene amaganiza bwino

22Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusiyana kwa zilankhulo zanu ndiponso maonekedwe a makungu anu. Ndithudi mu chimenechimulizizindikirokwaanthuophunzira

23Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kugona kumene mumagona usiku ndi usana kufunafuna chisomo chake. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro kwa anthu amene amatha kumva

24Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti Iye amakuonetsani mphezi imene imakuchititsani mantha ndiponso kukupatsani chikhulupiriro. Ndipo amatumiza mvula kuchokera ku mitambo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndithudi mu chimenechi muli zizndikiro kwa anthu ozindikira

25Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti kumwamba ndi dziko lapansi zimadzichepetsa potsatira malamulo ake ndipo pamene Iye akuitanani inu kamodzi kokha kuchokera m’nthaka, Taonani inu mudzadza mwamsanga msanga

26Ndipo chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi ndi chake ndipo zonse zimamumvera Iye

27Ndipo Iye ndiye amene amayambitsa chilengedwe ndipo adzachibwerezanso ndipo zimenezi ndi zapafupi kwa Iye. Ndipo wake ndi ulemerero kumwamba ndi padziko lapansi. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse

28Iye ali kupereka chitsanzo chokhudza inu nomwe. Kodi inu muli nawo akapolo amene amakhala anzanu pa zinthu zimene takupatsani ndipo kuti mumagawana nawo zinthuzo mofanana ndiponso mumawaopa iwo monga momwe mumaoperana? Mmenemo ndi mmene timasiyanitsira chiphunzitso chathu kwa anthu amene amazindikira

29Iyayi! onse osalungama amatsatira zilakolako zawo mosadziwa. Kotero ndani angatsogolere iye amene Mulungu wamusocheretsa? Ndipo iwo sadzakhala ndi wowathandiza

30Kotero dzipereke kwathunthu ku chipembedzo choonadi, chipembedzo, chenicheni, chimene Mulungu adalamula kuti munthu ayenera kutsatira. Chilengedwe chimene Mulungu adalenga mtundu wa anthu sichingasinthidwe. Ndithudi pali Mulungu, icho ndicho chipembedzo choona. Koma ambiri a mtundu wa anthu sadziwa

31Lapani kwa Iye ndiponso muopeni Iye. Pitirizani kupemphera nthawi zonse ndipo musakhale inu pakati pa iwo amene amafanizira milungu ina ndi Mulungu weniweni

32Pali anthu amene amagawa chipembedzo chawo ndi kukhala mipingo yosiyanasiyana ndipo mpingo uliwonse umasangalala ndi zimene uli nazo

33Ndipo pamene mavuto adza pa anthu, iwo amalira kwa Ambuye wawo ndi kudza kwa Iye modzichepetsa. Koma pamene Mulungu awaonetsa gawo lachisoni chochokera kwa Iye Mwini, ena a iwo amayamba kupembedza milungu ina yoonjezera pa Ambuye wawo

34Akhala ngati ali kuonetsakusathokozapazimenetawachitira. Basangalalani mwa kanthawi kochepa ndipo posachedwapa mudzadziwa kupusa kwanu

35Kodi kapena Ife tidawatumizira lamulo limene limanena za zinthu zimene iwo amazipembedza zoonjezera pa Mulungu

36Ndipo pamene tiwaonetsera anthu chifundo chathu, iwo amasangalala kwambiri chifukwa cha chifundocho ndipo ngati choipa chidza pa iwo chifukwa cha zimene iwo achita ndi manja awo, taonani! Iwo amadandaula kwambiri

37Kodi iwo saona kuti Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndiponso zomupatsazochepa munthu yemwe wamufuna. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro kwa anthu okhulupirira

38Kotero apatseni zosowa zawo abale anu, anthu osauka ndi a paulendo. Ichi ndicho chinthu chabwino kwambiri kwa iwo amene afuna chisangalalo cha Mulungu ndipo awa ndiwo amene ali opambana

39Chimene mumapereka ngati chiongoladzanja kuti chionjezere chuma cha anthu, sichidzakhala ndi chionjezero kwa Mulungu. Koma zopereka zimene mupereka ngati chaulere ndi cholinga chopeza madalitso a Mulungu ndi chimenechi chimene chidzaonjezeredwa kwambirimbiri

40Ndi Mulungu amene anakulengani inu amene amakupatsani zofuna zanu. Iye adzakonza kuti mufe patsogolopakepanondipokenakaadzakupatsaninsomoyo. Kodi chilipo china chilichonse chimene mungachifanizire ndi chimene chingachite zimenezi? Ulemerero ukhale kwa Iye ndipo Iye akhale zopambana kuposa zonse zimene amazifanizira ndi Iye

41Zinthu zoipa zalowa m’dziko ndiponso m’nyanja chifukwa cha ntchito za anthu zimene amachita ndi manja awo. Mulungu akhoza kuwalawitsa chilango chifukwa cha ntchito zawo kuti mwina athe kutembenuka

42Nena “Pitani paliponse pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale. Ambiri a iwo adali opembedza mafano.”

43Kotero dziperekeni kwathunthu ku chipembedzo choona lisanadze tsiku loopsa kuchokera kwa Mulungu limene silidzatheka kulizemba. Pa tsiku limeneli anthu adzagawidwa m’magulu

44onse osakhulupirira adzalangidwa chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndipo onse amene amachita ntchito zabwino adzadzisungira zinthu zabwino kumwamba

45Ndipo Iye adzawapatsa malipiro abwino onse amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuchokera ku zokoma zake. Ndipo Iye sakonda anthu osakhulupirira

46Ndipo chimodzi mwa zizindikiro zake ndi chakuti amatumiza mphepo imene imabweretsa zabwino ndi cholinga choti mulawe chisomo chake ndiponso kuti zombo ziyende mwamalamulo ake ndiponso kuti inu muzifunafuna chifundo chake ndi kumuthokoza

47Ndithudi Ife tidatumiza, Atumwi kwa anthu awo iwe usanabadwe ndipo iwo adadza kwa iwo ndi chiphunzitso choyenera. Ife tidapereka chilango kwa anthu ochimwa ndipo kuthandiza anthu okhulupirira ndi udindo wosatha kwa Ife

48Mulungu ndiye amene amatumiza mphepo kuti iyendetse mtambo ndipo amaumwaza mlengalenga monga momwe wafunira. Iye amauphwanya ndipo inu mumaona mvula ili kugwa kuchokera mu mtambowo. Iye amagwetsa mvula pa akapolo ake amene wawafuna. Taonani! Iwo amakhala osangalala

49Ngakhale kuti, iyo isanadze, iwo anali kuda nkhawa

50Taonani zizindikiro za chisoni cha Mulungu mmene amaperekera moyo ku nthaka imene inali yakufa. Ndithudi Iye adzadzutsa zakufa kuti zikhale zamoyo. Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

51Ndipo ngati Ife tikatumiza mphepo imene imapangitsa mbewu zawo kusanduka za chikasu, iwo amakhala osathokoza

52Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu wosamva kuti amve kuitana pamene iwo atembenuka ndi kuthawa

53Ndipo iwe siungathe kumutsogolera munthu wakhungu kuti asiye kulakwa kwake. Palibe amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chiphunzitso chathu

54di Mulungu amene adakulengani inu ofoka ndipo adakupatsani mphamvu pambuyo pa kufoka. Ndipo atakupatsani mphamvu adakupatsani kufoka ndi imvi. Iye amalenga chilichonse chimene wafuna ndipo ndiye amene amadziwa zonse ndipo ndiye Mwini mphamvu

55Ndipo pamene ola lidzadza, anthu ochimwa adzalumbira kuti adangokhala ola limodzi lokha. Kotero iwo amakhala onamizidwa

56Ndipo iwo amene adapatsidwa nzeru ndi chikhulupiriro adzati, “Ndithudi inu mwakhala molingana ndi malamulo a Mulungu mpaka pa tsiku louka kwa akufa. Kotero ili ndilo tsiku louka kwa akufa koma inu simunalidziwe ayi.”

57Koma patsiku limeneli zodandaula zawo sizidzawathandiza anthu onse ochimwa ndipo sizidzamveka ayi

58Ndithudi m’Buku ili la Korani anthu tawaikiramo zitsanzo zambiri zosiyanasiyana ndipo ngati iwe utawabweretsera chiphunzitso iwo amene sakhulupirira adzati, “Iwe siuli kutsatira china chilichonse koma bodza ndi matsenga.”

59Mmenemo ndi mmene Mulungu amatsekera mitima ya anthu osadziwa

60Kotero pirirani. Lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo usalole anthu opanda chikhulupiriro kuti akuderere iwe

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath