Chisilamu
kubwerera

29. Al-Ankaboot

1Alif. Lam Mim

2Kodi anthu amaganiza kuti adzasiyidwa okha osayesedwa chifukwa anena kuti, “Ife ndife okhulupirira?”

3Ndipo ndithudi Ife tidawayesa anthu amene adalipo iwo asanadze. Ndithudi Mulungu adzawazindikira iwo amene ndi olungama, ndipo ndithudi, adzawazindikira iwo amene ndi abodza

4Kodi kapena iwo amene amachita zoipa amaganiza kuti adzatithawa ife? Iwo amaweruza molakwa

5Aliyense amene amakhulupirira kuti adzakumana ndi Mulungu nthawi imene Mulungu adakhazikitsa, ndithudi, idzabwera ndipo Iye ndi wakumva ndi wodziwa

6Ndipo aliyense amene adzipereka kwathunthu, akudzipereka podzithandiza iye mwini. Ndithudi Mulungu ndi woima payekha ndipo Iye safuna thandizo lochokera kwa zolengedwa zake

7Ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ife tidzawakhululukira machimo awo ndikuwapatsa malipiro ofanana ndi ntchito zawo zabwino

8Ndipo Ife tidamulamula munthu kuonetsa ubwino kwa makolo ake koma ngati iwo akuuza kuti uzindiphatikiza Ine ndi ena ake amene iwe siuwazindikira, usawamvere ayi. Kwa Ine ndiko mudzabwerera ndipo ndidzakuuzani zimene munali kuchita

9Ndipo iwo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, ndithudi, Ife tidzawaika m’gulu la anthu angwiro

10Ndipo pakati pa anthu pali iye amene amati, “Ife timakhulupirira mwa Mulungu.” Koma akangoona mavuto chifukwa chodzipereka kwa Mulungu, amaganiza kuti kuponderezedwa kwawo ndi anthu ndi mkwiyo wochokera kwa Mulungu! Ndipo ngati thandizo lidza kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako, ndithudi, iwo adzati, “Ife tidali kumbali yako.” Kodi mukuganiza kuti Mulungu sadziwa zonse zimene zili m’mitima mwawo pakati pa zolengedwa zake zonse

11Ndithudi Mulungu amawadziwa anthu onse okhulupirira ndi anthu onse a chinyengo

12Ndipo anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Tsatirani njira yathu ndipo ife tidzavomera chilango chifukwa cha kuchimwa kwanu. Iwo sadzavomera chilango china chilichonse m’malo mwawo. Ndithudi iwo ndi abodza

13Iwo adzanyamula mtolo wawo pamodzi ndi mitolo ina ndi yawo. Ndipo patsiku lachiweruzo iwo adzafunsidwa kufotokoza mabodza awo

14Ndipo ndithudi tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo adakhala pakati pawo zaka chikwi chimodzi kuchotsapo zaka makumi asanu. Ndipo chigumula chidawapeza ali pa uchimo

15Kotero tidamupulumutsa iye pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo ndipo tidachipanga icho kukhala phunziro kwa anthu a mitundu yonse

16Ndipo Ife tidamupulumutsa Abrahamu pamene adati kwa anthu ake, “Pembedzani Mulungu ndipo muzimuopa Iye. Chimenecho chidzakhala chinthu chabwino kwa inu ngati mukadazindikira.”

17Chifukwa inu mumapembedza mafano oonjezera pa Mulungu ndipo inu mumapeka bodza. Zinthu zimene mumapembedza zoonjezera pa Mulungu zilibemphamvuzokupatsanizofunazanu.Koteropemphani zofuna zanu kwa Mulungu ndipo muzimuthokoza Iye. Kwa Iye ndiko kumene mudzabwerera

18Ndipo ngati inu mukana uthenga dziwani kuti nawonso amene adalipo inu musanadze adachita chimodzimodzi. Ndipo udindo wa Mtumwi ndi kulalikira pagulu momveka

19Iwo sakuona mmene Mulungu amayambitsira chilengedwe ndiponso mmene amachibwerezanso. Ndithudi zimenezo ndi za pafupi kwa Mulungu

20Nena, “Yendani paliponse pa dziko lapansi ndipo muone mmene Mulungu adayambitsira chilengedwe. Kotero Mulungu adzalenga chilengedwe chinanso. Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse.”

21Iye amalanga aliyense amene wamufuna ndiponso amaonetsa chifundo chake kwa aliyense amene wamufuna. Ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera

22Kaya ndi pa dziko lapansi kapena kumwamba, kulibe kumene inu mungathawire. Ndipo inu mulibe wina kupatula Mulungu amene angakutetezeni kapena kukuthandizani

23onse amene amakana zizindikiro za Mulungu ndiponso zokumana naye m’moyo umene uli nkudza ndiwo amene amakayika za chifundo changa. Ndipo iwo adzalandira chilango chowawa kwambiri

24Yankho la anthu a Abrahamu lidali lamwano ndipo adati, “Mumuphe kapena mumutenthe.” Koma Mulungu adamupulumutsa iye ku moto. Ndithudi mu zimenezi muli phunziro kwa anthu okhulupirira

25Ndipo iye adati, “Inu mwasankha kupembedza mafano kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa chokweza mgwirizano wa pakati panu m’moyo uno. Koma pa tsiku lachiweruzo inu mudzakanana wina ndi mnzake. Ndipo malo anu akakhala ku moto ndipo inu simudzakhala ndi wina wokuthandizani.”

26Koma Loti adamukhulupirira iye. Iye adati, “Ndidzachoka pa nyumba yanga chifukwa cha Ambuye wanga chifukwa Iye ndi wamphamvu zambiri ndi wanzeru.”

27Ndipo tidamupatsa Abrahamu, Isake ndiYakobo ndipo tidakhazikitsa pakati pa ana ake utumiki ndi chivumbulutso. Ndipo Ife tidamupatsa mphotho yake m’moyo uno ndipo iye adzakhala m’moyo umene uli nkudza, pagulu la anthu olungama

28Ndipo tidatumiza Loti, kotero iye adati kwa anthu ake, “Inu muli kuchita zinthu zonyansa zimene sizidachitikeponso ndi mtundu wa anthu kuyambira kalekale.”

29“Kodi inu mumakaputa anthu a aamuna ndi kuchita chifwamba m’misewu ndiponso mumaphunzitsa zoipa ngakhale m’magulu anu?” Iwo sadayankhe china chilichonse kupatula kuti iwo adati, “Bweretsa pa ife chilango cha Mulungu ngati iwe ukunena zoona.”

30Iye adati, “Ambuye wanga! Thandizeni polimbana ndi anthu oipawa.”

31Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Abrahamu, ndi nkhani ya bwino, iwo adati, “Ndithudi ife tidzaononga anthu a mu mzinda uno chifukwa anthu ake ndi osalungama.”

32Iye adati, “Ndithudi mu mzindamo muli Loti.” Iwo adati, “Ife tikudziwa amene ali m’menemo. Ndithudi ife tidzamupulumutsa iye ndi omutsatira ake onse kupatula mkazi wake. Iye adzakhala m’gulu la anthu otsalira.”

33Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Loti, iye anada nkhawa pa zimene zingawachitikire iwo ndipo iye adaoneka wopanda mphamvu yowateteza iwo. Ndipo iwo adati, “Usaope kapena kuda nkhawa. Ndithudi ife tidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi okutsatira ako kupatula mkazi wako. Iye adzakhala m’gulu la anthu otsalira.”

34Ndithudi Ife tidzatsitsa chilango kuchokera kumwamba, kuti chilange anthu a mzinda uno chifukwa cha machimo awo

35Ndithudi Ife tasiya chiphunzitso chokwanira kwa anthu ozindikira

36Ndipo kwa anthu a ku Midiyani tidatumiza m’bale wawo Shaibu ndipo iye adati, “oh anthu anga! Tumikirani Mulungu ndipo opani tsiku limene lili nkudza ndipo musayambitse chisokonezo m’dziko pochita zinthu zoipa.”

37Koma iwo adamukana iye, kotero chivomezi chachikulu chidadza pa iwo ndipo mitembo yawo idali lambilambi m’nyumba zawo

38Ndi Aad ndi Thamoud. Chitsimikizo chake chili m’mabanja a m’mizindayi. Satana adawapangitsa kuganiza kuti ntchito zawo zoipa zidali zabwino ndipo iye adawabweza ku njira yoyenera ngakhale kuti iwo adali anthu anzeru ndi aluntha

39Ndipo Ife tidaononga Karuni, Farawo ndi Hamani. Ndithudi Mose adadza kwa iwo ndi chiphunzitso chabwino koma iwo anali kukhala mwamwano m’dziko ngakhale kuti iwo sakadatha kutigonjetsa Ife

40Kotero tidalanga aliyense chifukwa cha machimo ake. Pakati pa iwo padali iwo amene tidawatumizira mvula yamkuntho, ndipo pakati pawo padali iwo amene adavutika ndi mphenzi, ndipo pakati pawo padalinso iwo amene adamezedwa ndi nthaka ndipo padalinso iwo amene tidawamiza ndipo Mulungu sadalakwe ayi koma iwo ndiwo amene adalakwira mizimu yawo

41Fanizo la iwo amene amasankha owateteza kuonjezera pa Mulungu ndi Kangaude amene amamanga nyumba yake yaulusi. Ndipo ndithudi iwo akadayenera kudziwa kuti nyumba ya Kangaude ndi imodzi mwa nyumba zosalimba

42Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene iwo amapembedza kuonjezera pa Iye ndipo Iye ndi wamphamvu ndi wanzeru

43Ndipo zitsanzozi tili kuziulula chifukwa cha anthu koma palibe amene amazizindikira koma ophunzira okha

44Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi. Ndithudi muli phunziro mu zimenezi kwa anthu okhulupirira

45Lakatula zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera m’Bukundipopitirizakupemphera. Ndithudimapemphero amateteza munthu ku machimo ndi zinthu zoipa. Ndithudi kukumbukira Mulungu ndi chinthu chachikulu ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita

46Ndipo musatsutsane ndi anthu okhulupirira za m’Buku pokhapokha kutakhala koyenera kutero, kupatula okhawo amene amachita zoipa. Nena, “Ife timakhulupirira mu izo zimene zavumbulutsidwa kwa ife ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa inu ndipo Mulungu wathu ndi Mulungu wanu ndi mmodzi ndipo ife tadzipereka kwa Iye.”

47Ndipokotero Ifetavumbulutsa Bukulolemekezekakwa iwe. Kotero onse amene tawapatsa Buku amakhulupirira mwa ilo ndipo palibe amene amakana chivumbulutso chathu kupatula anthu osalungama

48Ndipo iwe siudalakatule za m’Buku lina ili lisanadze. Ndipo iwe siudalembe Buku lina lililonse ndi manja ako. Zikadatero, ndithudi, anthu oyankhula zachabechabe akadakayika

49Iyayi! Izi ndi ziphunzitso zomveka zimene zili m’mitima ya iwo amene adapatsidwa nzeru ndipo palibe amene amakana chiphunzitso chathu kupatula wosalungama

50Iwo amati, “Bwanji Ambuye wake sadamupatse zizindikiro?” Nena, ” Zizindikiro zonse zili ndi Mulungu ndipo ine ndine mchenjezi chabe.”

51Kodi sizidakwanire kuti tavumbulutsa Buku lolemekezeka kwa iwe limene lili kuwerengedwa kwa iwo? Ndithudi m’Bukuli muli chifundo ndi chikumbutso kwa anthu okhulupirira

52Nena, “Mulungu ndi mboni yokwana pakati pa ine ndi inu. Iye amadziwa chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi.” Ndipo iwo amene amakhulupirira zabodza, ndiponso sakhulupirira mwa Mulungu, amenewa, ndi anthu olephera

53Iwo amakukakamiza kuti ubweretse chilango msanga. Ndipo zikadakhala kuti nthawi yake siidakhazikitsidwe kale, ndithudi, chilango chikadakhala chitadza kale pa iwo. Ndithudi icho chidzadza pa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sali kuchiganizira

54Iwo ali kukukakamiza kuti ubweretse chilango. Ndithudi Gahena idzadzadza ndi anthu osakhulupirira

55Patsiku limene chilango chidzadza pa iwo kuchokera kumwamba ndi padziko lapansi mawu adzati, “Lawani inu zipatso za ntchito zanu.”

56oh inu akapolo anga amene mwakhulupirira! Ndithudi dziko langa lili ndi malo ambiri. Kotero ndipembedzeni Ine ndekha

57Mzimu uliwonse udzalawa imfa. Pomaliza nonse mudzabwererakwa Ife

58Ndipoiwoameneamakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, otere tidzawapatsa malo kumwamba amene pansi pake pamayenda mitsinje kuti akhale m’menemo mpaka kale kale. Eti kukoma mphotho ya iwo amene amachita zabwino

59Iwo amapirira ndipo amaika chikhulupiriro chawo mwa Ambuye wawo ndi Mtetezi wawo

60Kodi zilipo zolengedwa zingati zimene sizisunga chakudya chawo? Ndi Mulungu amene amazidyetsa izo pamodzi ndi inu nomwe. Ndipo Iye ndi wakumva ndi wodziwa

61Ndithudi ngati iwe utawafunsa kuti kodi ndani amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndiponso amene adalamula dzuwa ndi mwezi kumvera malamulo ake? Ndithudi iwo adzayankha kuti ndi Mulungu. Nanga ndi chifukwa chiyani iwo amakana choonadi

62Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndipo amamana aliyense amene Iye wamufuna. Ndithudi Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse

63Ngati iwe ungawafunse kuti kodi ndani amene amagwetsa mvula ndipo amapereka moyo ku nthaka imene idali ya kufa? Ndithudi iwo adzayankha kuti, “Ndi Mulungu.” Nena “Kuyamikidwa konse kukhale kwa Iye.” Iyayi, ambiri a iwo sazindikira

64Ndipo moyo wa padziko lapansi siuli kanthu koma masewera ndi kongotayira nthawi. Ukakhala moyo umene uli nkudza, umenewo ndiwo weniweni, iwo akadadziwa

65Kotero iwo akamakwera zombo amapempha kwa Mulungu modzipereka ndi modzichepetsa. Koma Iye akawafikitsa pa mtunda mwaubwino, Ah! iwo amamufanizira Iye ndi zina zake

66Kotero iwo amaonetsa kusathokoza pa zimene tawapatsa kuti akhoza kusangalala; ndipo iwo adzazindikira posachedwapa

67Kodi iwo saona kuti tateteza malo odalitsika pamene anthu ena ali kutengedwa mwankhanza pa malo owazungulira? Kodi iwo adzakhala ali kukhulupirirabe zabodza ndi kukana ubwino wa Mulungu

68Kodi woipitsitsa ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amene amati choonadi ndi chabodza pamene auzidwa za icho? Kodi Gahena siidzakhala malo okhalamo anthu onse osakhulupirira

69Akakhala iwo amene amalimbikira kugwira ntchito yathu,ndithudi, Ife tidzawatsogolera ku njira zathu. Ndithudi Mulungu amakhala ndi iwo amene amachita zabwino

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath