Chisilamu
kubwerera

28. Al-Qasas

1Ta Sin Mim

2Awa ndi mawu a m’Buku lofotokoza bwino

3Tidzakuuza zina za mbiri ya Mose ndi Farawo mwachoonadi kuti uuze anthu okhulupirira

4Ndithudi Farawo adadzikweza pa dziko lapansi ndipo adagawa anthu ake m’magulumagulu ndipo gulu lina iye anali kulizunza pomapha ana awo aamuna ndi kusiya ana aakazi. Ndithudi iye adali wochita zoipa

5Koma chidali chifuniro chathu kuti tiwapatse zabwino anthu amene adali oponderezedwa pa dziko ndi kuwasandutsa iwo kukhala atsogoleri a anthu ndi kuwapanga iwo kulowa m’malo mwa ufumu wa Farawo

6Ndikuwakhazikitsa m’dziko ndipo tinamupatsa Farawo, Hamani ndi gulu lawo la nkhondo zimene iwo anali kuopa

7Ife tidauza amayi ake a Mose ponena kuti, “Muyamwitse iye koma ngati ukuda nkhawa za kukhala kwake mwamtendere, mponye mu mtsinje. Usaope ndipo usade nkhawa ayi chifukwa Ife tidzamubweretsa iye kwa iwe ndi kumupanga iye kukhala mmodzi wa Atumwi.”

8Ndipo adamutola iye a banja la Farawo kuti akhoza kukhala mdani ndiponso madandaulo kwa iwo. Ndithudi Farawo, Hamani ndi Asirikali awo, onse adali ochimwa

9Mkazi wake wa Farawo adati kwa iye, “Mwana uyu akhoza kubweretsa chisangalalo kwa ine ndi iwe. Musamuphe ayi. Mwina akhoza kutithandiza kapena tikhoza kumutenga kuti akhale mwana wathu.” Koma iwo sadadziwe chimene anali kuchita

10Mtima wa amayi ake a Mose siumaganiza zina ayi koma za Mose yekha. Iye akadaulula za iye kukadapanda kuti Ife tidamupatsamphamvukutiapitirizekukhalawokhulupirira weniweni

11Iye adati kwa mlongo wake wa Mose, “Pita umutsatire.” Iye anali kumuona kuchokera patali pamene iwo sadadziwe ayi

12Tsopano Ife tidamupanga kuti azikana kuyamwa mawere a amayi ena. Mlongo wake adati kwa iwo, “Kodi ndingakulondorereni banja limene likhoza kumulera m’malo mwanu ndi kumusamala bwino?”

13Ndipo tidamubweretsa iye kwa Amayi ake kuti asangalale, asiye kudandaula ndiponso kuti adziwe kuti lonjezo la Mulungu ndi loona. Koma anthu ambiri sachidziwa chimenechi

14Ndipo pamene iye adakula msinkhu ndi kukhala munthu wokwana, tidamupatsa iye luntha ndi nzeru. Mmenemu ndi mmene timalipirira anthu ochita zabwino

15Ndipo Iye adalowa mu mzinda, osaonedwa ndi anthu ndipo adapeza anthu awiri ali kumenyana, wina adali wa mtundu wake ndi wina wa mtundu wa adani ake. Munthu wa mtundu wake adamupempha iye chithandizo kuti agonjetse mdani wake. Ndipo Mose adamumenya mdani wake ndi dzanja lake ndipo adamupha. Mose adati, “Iyi ndi ntchito ya Satana. Ndithudi Iye ndi mdani wa munthu wosokoneza kwenikweni.”

16Iye adati, “Ambuye! Ine ndidalakwira mzimu wanga kotero ndikhululukireni.” Ndipo Mulungu anamukhululukira iye chifukwa Iye ndi Mwini kukhululukira ndi Mwini chisoni chosatha

17Iye adati, “Chifukwa cha chifundo chimene mwandionetsa Ambuye, ine ndili kulumbira kuti sindidzathandiza wina aliyense wochita zoipa.”

18M’mawa mwake iye anali kuyenda mu mzinda ndi mantha poyembekezera mavuto. Munthu uja, amene amamuthandiza cha dzulo, adamuitananso kuti amuthandize. Mose adati, “Ndi choonekeratu kuti iwe ndiwe munthu wosokoneza.”

19Ndipo pamene Mose ankati azim’menya mdani uja, munthuyo adati, “Iwe Mose! Kodi ufuna kundipha monga momwe unaphera munthu uja dzulo? Ndithudi iwe ufuna kukhala munthu wankhanza m’dziko lino ndiponso iwe siufuna kukhala mmodzi mwa anthu angwiro.”

20Ndipo munthu wina adadza kuchokera ku malire a mzinda ali kuthamanga. Iye adati, “Mose! Anthu ndi mafumu ali kuchita upo woti akuphe iwe. Tuluka mu mzindawu. Ine ndili kukulangiza iwe mwachoonadi.”

21Iye adachoka ku Aiguputo mwamantha, ali kuyembekeza kuti zoipa zim’peza. Anali akunena kuti, “Ambuye, ndipulumutseni ku anthu oipa.”

22Ndipo pamene anali kuyandikira ku Midiyani Iye adati, “Ambuye anditsogolera ku njira yoyenera.”

23Ndipo pamene adafika pa chitsime cha ku Midiyani, iye adapeza gulu la anthu aamuna amene adali kumwetsa ziweto zawo. Ndipo kuonjezera paiwo, padali akazi awiri amene anali kungosunga nkhosa zawo. Mose adati, “Kodi vuto lanu ndi chiyani?” Iwo adati, “Sitingathe kumwetsa nkhosa zathu pokhapokha abusa awa atachotsa ziweto zawo. Ndipo bambo wathu ndi munthu wokalamba.”

24Mose adawamwetsera nkhosa zawo ndipo adachoka ndi kukakhala pa m’thunzi nati, “Ambuye, ine ndili kusowa zabwino zimene munganditumize.”

25Mmodzi mwa akazi aja adadza kwa iye akuyenda mwamanyazi nati, “Abambo anga ali kukuitanani kuti akakulipireni chifukwa chomwetsera ziweto zathu.” Ndipo pamene Mose adadza kwa iwo, adafotokoza nkhani yake kwa iye. Bambo uja adati, “Usaope. Tsopano wapulumuka m’manja mwa anthu oipa.”

26Mmodzi mwa akazi aja adati, “Atate, mulembeni ntchito munthu uyu. Munthu wabwino kumulemba ntchito ndi amene ali ndi mphamvu ndiponso wokhulupirika.”

27Atate adati, “Ine ndidzakupatsa mmodzi wa ana anga aakazi kuti umukwatire ngati ungakhale zaka zisanu ndi zitatu uli kundigwirira ntchito. Koma ngati ufuna ukhoza kugwira ntchito zaka khumi. Ine sindifuna kukuzunza ayi. Ngati Mulungu afuna, udzaona kuti ine ndine munthu wangwiro.”

28Mose adati, “Zimenezi zikhale pakati pa inu ndi ine. Mwa nthawi ziwirizi ine ndidzakwaniritsa ndipo pasadzakhale cholakwa kwa ine. Ndipo Mulungu ndi mboni pa zimene tili kukambiranazi.”

29Ndipo pamene adamaliza nthawi yake, iye anali kupita ndi mkazi wake. Mose adaona moto kuonjezera pa phiri la Sinai. Iye adati kwa mkazi wake, “Khala pano chifukwa ndili kuona moto. Mwina mwake ndikhoza kubweretsa kuchokera kumeneko nkhani kapena mwatso woyaka umene ukhoza kuotha.”

30Ndipo pamene adafika pamalo paja, iye adaitanidwa kuchokera kumbali ya manja ya chigwa pa malo odalitsika kuchokera mumtengo. “oh iwe Mose! Ndithudi, Ine ndine Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse.”

31“Ndipo ponya pansi ndodo yako.” Ndipo pamene adaona ndodo yake ili kuyenda ngati njoka, adatembenuka nathawa osabwevukanso. “Iwe Mose! Bwerera ndipo usaope. Iwe ndiwe mmodzi wa anthu otetezedwa.”

32“Ika dzanja lako m’thumba, ndipo ilo lidzakhala loyera kwambiri lopanda chilema ndipo ika dzanja lako pamtima pako kuti uchoke mantha. Kotero zimenezi ndi zizindikiro ziwiri za Ambuye wako kwa Farao ndi mafumu ake. Mosakaika iwo ndi anthu osakhulupirira.”

33Mose adati, “Ambuye wanga! Ine ndidapha mmodzi mwa anthu awo ndipo ndili ndi mantha kuti mwina akhoza kukandipha.”

34“Ndipo Aroni, m’bale wanga, amayankhula bwino kuposa ine. Mutumizeni iye pamodzi ndi ine kuti akhoza kukandithandiza kuti akandiyankhulire. Ndithudi ine ndiopa kuti akandikana.”

35Iye adati, “Ife tidzakuonjezera mphamvu pokhala ndi m’bale wako ndipo ndiika pa inu awiri umboni ndipo iwo sadzatha kukupwetekani inu chifukwa cha zizindikiro zathu. Inu pamodzi ndi onse amene amakutsatirani mudzapambana.”

36Ndipo pamene Mose adadza kwa iwo ndi zizindikiro zathu zooneka, iwo adati, “Izi si zina ayi koma matsenga ongopeka ndiponso ife sitidamvepo kuti za mtundu uwu zinachitikapo kuchokera kwa makolo athu akale.”

37Ndipo Mose adati, “Ambuye wanga amadziwa bwinobwino munthu amene amabweretsa chilangizo chochokera kwa Iye, ndiponso kwa amene tsogolo lake ndi labwino. Ndithudi anthu onse ochimwa sadzapambana ayi.”

38Farawo adati, “oh inu mafumu! Inu mulibe mulungu wina amene ine ndimudziwa kupatula ine ndekha. Haman, ndipangireni ine njerwa zadothi ndipo mundimangire nyumba yaitali, yonga nsanja, kuti ndikwerepo kupita kwa Mulungu wa Mose. Ndithudi ine ndili kumuganizira kuti Mose ndi mmodzi mwa anthu abodza.”

39Farawo ndi Asirikali ake adadzikweza kwambiri mu dziko la Aiguputo popanda chifukwa ndipo iwo anali kuganiza kuti sadzabwereranso kwa Ife

40Ndipo tidamutenga iye pamodzi ndi asirikali ake ndipo tidawamiza m’nyanja. Ganiza chimene amaona anthu ochita zoipa

41Ife tidawapanga iwo kukhala atsogoleri oitana anthu kuti apite kumoto koma pa tsiku la kuuka kwa akufa, palibe mmodzi amene adzawathandiza iwo

42Ife tidawatsatira ndi matemberero m’dziko lino ndipo pa tsiku la kuuka kwa akufa iwo adzakhala anthu onyozeka

43Ndipo ife tidaononga mibadwo yoyamba yakale ndipo tidamupatsa Mose Buku la Chipangano Chakale monga nyali, langizo ndi chifundo kwa anthu kuti mwina akhoza kuchenjezedwa

44Iwe kudalibe, ku mbali ya kumadzulo kwa phiri, pamene Ife tinali kumupatsa Mose udindo wake ndiponso iwe kunalibe pa mwambowu

45Koma Ife tidalenga mibadwo yambiri Mose atafa kale imene inali ndi moyo wautali. Iwe siunakhale pakati pa anthu a ku Midiyani ndi kumawalakatulira chivumbulutso chathu. Koma Ife ndi amene timatumiza Atumwi

46Ndipo iwe kudalibe m’mbali mwa phiri la Sinai pamene tidamuitana Mose. Koma adali madalitso ochokera kwa Ambuye wako kuti ukachenjeze mtundu wa anthu umene unalipo iwe usanadze kotero kuti akhoza kuchenjezedwa

47Tikanapanda kukutumiza iwe ndipo mazunzo akadawagwera chifukwa cha ntchito zawo zoipa, iwo akadati, “Ambuye, chifukwa chiyani simudatitumizire Mtumwi kotero kuti tikadatsatira mawu anu ndiponso tikadakhala okhulupirira.”

48Ndipo pamene choonadi chadza kwa iwo kuchokera kwa Ife, iwo ali kufunsa kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani iye sadapatsidwe monga zomwe zidapatsidwa kwa Mose?” Kodi iwo sadakane zimene zidapatsidwa kwa Mose kale? Iwo amati, “Zizindikiro ziwiri za matsenga zili zothandizana.” Ndiponso amanena, “Ife sitidzakhulupirira mu china chilichonse cha zimenezi.”

49Nena, “Bweretsani Buku lochokera kwa Mulungu limene lili ndi langizo labwino kuposa malangizo awa ndipo ine ndidzatsatira ngati zimene muli kunena ndi zoona.”

50Ngati iwo akanika kukuyankha, dziwa kuti iwo ali kutsatira zilakolako zawo. Kodi ndani amene ali wolakwa kwambiri kuposa munthu amene amatsatira zilakolako zake opanda langizo la Mulungu? Ndithudi Mulungu satsogolera anthu olakwa

51Ndithudi tatumiza mawu athu motsatana kwa iwo kuti akhoze kuchenjezedwa

52Iwo amene kale tidawapatsa Buku lino lisadadze, amakhulupirira mwa ilo

53Pamene limalakatulidwa kwa iwo, amati iwowo “Ife tili kulikhulupirira Bukuli chifukwa ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wathu. Ife tidadzipereka kwathunthu kalekale mawu awa asadadze.”

54Anthu awa mphotho yawo idzaperekedwa kwa iwo kawiri chifukwa iwo adapirira ndipo amagonjetsa choipa pochita chabwino ndi kumapereka gawo la chaulere pa katundu amene tidawapatsa

55Ndipo iwo akamva mawu oipa, salabadira zonenazo koma amati, “Ife tili ndi ntchito zathu ndipo nanunso muli ndi ntchito zanu. Mtendere ukhale kwa inu. Ife sitifuna kugwirizana ndi anthu osadziwa.”

56Iwe siungamutsogolere aliyense amene umufuna. Ndi Mulungu yekha amene amatsogolera aliyense amene Iye wamufuna. Iye amadziwa bwino anthu amene ali oyenera

57Iwo amati, “Ngati ife titsatira chilangizo chako, ife tikuopakulandidwadzikolathu.”KodiIfesitidawakhazikire malo otetezedwa kumene zipatso za mtundu uliwonse zimaperekedwa ngati chakudya kuchokera kwa Ife? Ndithudi ambiri a iwo ndi anthu osadziwa

58Kodi ndi mizinda ingati imene tidaononga imene idali kunyada chifukwa cha chuma chake? Kotero zimenezi ndizo nyumba zawo zimene sadakhalitsemo ndipo tsopano eni ake ndife

59Ndipo Ambuye wako sadaononge mizinda mpaka pamene Iye adadzutsa kuchokera mu iyo, Mtumwi amene amalalikira za chivumbulutso chathu ndipo Ife sitidzaononga mzinda pokhapokha anthu okhala mmenemo ali olakwa

60Zinthu zimene mwapatsidwa si zina koma chakudya ndiponso chionetsero chopanda pake cha m’moyo uno. Koma chimene chili ndi Mulungu ndicho chabwino ndiponso chokhalitsa. Kodi simungathe kuzindikira

61Kodi anthu awiriwa ndi ofanana? Iye amene tamulonjeza lonjezo labwino ndipo adzalikwaniritsa ndi iye amene tamupatsa zokoma zambiri za m’moyo uno koma pa tsiku lachiweruzo adzakhala m’gulu la iwo olangidwa

62Pa tsiku limeneli Mulungu adzawaitana ndipo adzati, “Kodi aja munkati ndi anzanga ali kuti?”

63Iwo amene adzapezeka ndi mlandu wotere adzati, “Awa ndiwo anthu amene ife tidawasocheretsa. Ife tidawasocheretsa chifukwa nafenso tidali osochera. Ife tsopano tadzipatula (kuchoka mwa iwo) ndi kudza kwa inu. Si ndife amene iwo anali kupembedza.”

64Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti, “Itanani anzanu kuti akuthandizeni.” Iwo adzawaitana koma iwo sadzawamva ayi. Ndipo iwo adzalawa chilango chowawa. Iwo adzafunitsitsa akadatsogozedwa bwino

65Tsiku limene Mulungu adzawaitana nati, “Kodi inu mudanena zotani kwa Mtumwi?”

66Zodandaula zawo sizidzamveka ayi, kotero sadzatha kufunsana wina ndi mnzake

67Akakhala iye amene alapa zoipa zake nakhulupirira ndipo achita ntchito zabwino, mwina akhoza kudzakhala pakati pa anthu opambana

68Ndipo Ambuye wako amalenga ndi kusankha aliyense amene Iye wamufuna. Kusankha si kwawo ayi. Ulemerero ukhale kwa Mulungu ndipo Iye atalikirane ndi zimene amamufanizira nazo

69Ambuye wako amadziwa zonse zimene amazibisa m’mitima mwawo ndiponso zimene amaziulula

70Iye ndi Mulungu ndipo palibenso mulungu wina koma Iye yekha. Kuyamikidwa konse ndi kwake m’moyo uno ndiponso m’moyo umene uli nkudza. Ndipo chake ndi chiweruzo ndipo kwa Iye mudzabwerera

71Nena, “Ndiuzeni! Ngati Mulungu atapanga usiku kuti usache mpaka pa tsiku louka kwa akufa, kodi ndi mulungu uti kupatula Mulungu weniweni amene akhoza kukupatsani usana? Kodi simukumva?”

72Nena, “Ndiuzeni! Ngati Mulungu atapanga usana kuti kusade mpaka pa tsiku louka kwa akufa, kodi ndi mulungu uti kupatula Mulungu weniweni amene akhoza kukupatsani usiku umene inu mumapumulamo? Kodi inu simukuona?”

73Mwachifundo chake wakupatsani usiku ndi usana kuti muzipezamo mpumulo ndi kufunafuna chisomo chake ndi kuti muzithokoza

74Ndipo pa tsiku limene adzawaitana iwo nati, “Kodi ali kuti iwo amene mumaganiza kuti ndi anzanga?”

75Ndipo nthawi yomweyo tidzaitana mboni kuchokera ku mtundu uliwonse ndipo tidzati, “Bweretsani umboni wanu.” Nthawi imeneyo adzadziwa kuti mwini wake choonadi ndi Mulungu ndipo zonse zimene amapeka zidzawathawira

76Ndithudi Karuni, mosakayika, adali wa ku mtundu wa Mose. Koma iye amawanyoza iwo chifukwa Ife tidamupatsa nkhokwe za chuma zimene ndithudi makiyi ake samatheka kunyamulidwa ndi anthu angapo a mphamvu. Anthu ake adati kwa iye, “Usadzikundikire chifukwa Mulungu sakonda anthu odzikundikira chifukwa cha chuma.”

77“Koma ufunefune, kudzera m’zimene Mulungu wakupatsa iwe, kuti upeze moyo umene uli nkudza, ndiponso usaiwale udindo wako m’dziko lino. Khala wabwino monga Mulungu wakuonetsera ubwino wake. Ndipo usalimbike pochita zoipa padziko lapansi chifukwa Mulungu sakonda anthu ochita zoipa.”

78Iye adati, “Chuma ichi chidapatsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru zanga.” Kodi iye sadadziwe kuti Mulungu adaononga m’badwo wonse wa anthu amene adali ndi mphamvu zambiri ndiponso olemera kwambiri iye asanabadwe? Anthu ochita zoipa sadzafunsidwa za machimo awo

79Kotero iye adapita kwa anthu ake monyadira atavala bwino. Anthu amene adali kukonda moyo wa pa dziko lapansi adati, “Tikadakhala kuti tidali nazo ngati zinthu zimene zili ndi Karuni! Ndithudi iye ndi wolemera kwambiri.”

80Koma iye amene adapatsidwa nzeru adati: “Tsoka kwa inu! Mphotho ya Mulungu m’moyo umene uli nkudza ndi yabwino kwa iwo amene amakhulupirira ndipo amachita zabwino.” Koma mphothoyo palibe amene adzailandira kupatula okhawo amene amapirira

81Kotero Ife tidalamulira nthaka kuti imumeze Karuni pamodzi ndi chuma chake ndipo sadapeze wina womuthandiza kwa Mulungu ndipo iye sadathe kudziteteza

82Ndipo iwo amene anali kukhumbira chuma chake chadzulo adayamba kunena kuti, “Taonani! Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene wamufuna ndi monyalapsa kwa aliyense amene Iye wamufuna. Akadakhala kuti sadatilangize ife chisoni chake, Iye akadalamulira nthaka kuti itimeze. Taonani! anthu okana Mulungu sadzakhala opambana ngakhale pang’ono.”

83Kunena za m’moyo umene uli nkudza, udzakhala wa iwo amene sadzikweza pa dziko lapansi kapena kuchita zoipa. Ndipo mapeto abwino ndi a iwo amene ali angwiro

84Aliyense amene achita zabwino adzalipidwa zochuluka. Koma iye amene achita zoipa ndiponso iwo amene achita ntchito zoipa adzangolipidwa molingana ndi zimene anali kuchita

85Ndithudi Iye amene adalamulira Buku la Korani kuti livumbulutsidwe kwa iwe adzakubwezera kumalo komwe udzapite. Nena, “Ambuye wanga adziwa bwino iye amene amabweretsa langizo loonadi ndiponso iye amene ndi wosochera.”

86Ndipo iwe siumayembekezera kuti Buku lolemekezeka lidzavumbulitsidwa kwa iwe koma ndi chifundo chochokera kwa Ambuye wako. Kotero usavomereze zochita za anthu omwe ali osakhulupirira

87Usalole wina aliyense kuti akubweze ku chivumbulutso cha Mulungu pamene chavumbulutsidwa kwa iwe ndipo aitane anthu kuti adze kwa Ambuye wako ndipo usakhale m’gulu la anthu amene amaphatikiza milungu ina ndi Mulungu weniweni

88Ndipo usamphatikize mulungu wina ndi Mulungu weniweni. Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Zinthu zonse ndi zakutha kupatula Iye yekha. Chake ndi chiweruzo ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath