Chisilamu
kubwerera

27. An-Naml

1Ichi ndi chivumbulutso cha Korani, Buku lofotokoza bwino

2Malangizo ndi nkhani yosangalatsa kwa anthu okhulupirira

3Amene amapitiriza kupemphera ndipo amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndiponso amakhulupirira kwambiri m’moyo umene uli nkudza

4Ndithudi iwo ndi amene amakana za moyo umene uli nkudza. Ife tazipanga ntchito zawo kuti zioneke ngati zabwino motero iwo amayenda mwakhungu

5Iwo adzalangidwa koposa. Ndipo m’moyo umene uli nkudza, iwo sadzapindula china chilichonse

6Ndithudi iwe walandira Korani kuchokera kwa Iye amene ali ndi nzeru ndipo amadziwa chilichonse

7Pamenepo Mose adauza banja lake kuti, “Ine ndili kuona moto. Ine posachedwapa ndikubweretserani nkhani kapena khala la moto kuti mukhoza kuotha.”

8Ndipo pamene iye adafika pamoto paja, mawu adamveka akunena naye kuti, “odalitsidwa ndiye amene ali mu moto uwu ndiponso alionse a pamalo pozungulira. Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse.”

9“Mose! Ine ndine Mulungu, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse.”

10“Ponya ndodo yako pansi.” Ndipo pamene iye adaona kuti ilikuyenda ngati njoka, adatembenuka ndi kuthawa ndipo sadayang’ane m’mbuyo. “Iwe Mose!” Atumwi anga sachita mantha pamene ali ndi Ine

11Akakhala iwo amene amalakwa ndipo amachita zabwino pambuyo pochita zoipa Ine ndine wokhululukira ndiponso wachisoni chosatha

12“Pisa dzanja m’thumba mwako. Litulutse lili loyera ngakhale kuti siudapweteke. Ichi ndi chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi zinayi zimene zidzaonetsedwa kwa Farawo ndi anthu ake. Ndithudi iwo ndi anthu ochimwa kwambiri.”

13Pamene zizindikiro zathu zooneka bwino zinaonetsedwa kwa iwo, iwo adati, “Uwu ndiwo ufiti weniweni.”

14Mitima yawo idadziwa kuti zizindikiro zidali zoona koma adazikana izo chifukwa chakulakwa ndiponso kunyada kwawo. Taona zimene zidawaonekera anthu olakwa

15Ndithudi Ife tidapereka nzeru kwa Davide ndi Solomoni. Iwo adati, “Kuyamikidwa ndi kwa Iye amene watikweza ife kukhala pamwamba pa akapolo ake ambiri okhulupirira.”

16Solomoniadalowam’malomwaDavide.Iye adati, “Oh inu anthu anga! Ife taphunzitsidwa chiyankhulo cha mbalame ndipo tapatsidwa zinthu zabwino zambiri. Ndithudi ichi ndi chifundo choonekeratu.”

17Asirikali a nkhondo a mtundu wa majini, anthu ena ndi mbalame anasonkhanitsidwa pamaso pa Solomoni ndipo adaimitsidwa pa mizere m’magulu osiyanasiyana mogwirizana ndi maudindo

18Mpaka pamene iwo anafika pa chigwa cha nyerere, nyerere ina idati, “Oh inu nyerere! Lowani ku maenje anu chifukwa mwina Solomoni pamodzi ndi Asirikali ake, akhoza kukuonongani mosadziwa.”

19Solomoni adamwetulira posangalatsidwa ndi mawu ake ndipo iye adati, “Ndilangizeni Ambuye kuti ndizikuthokozani pa zabwino zonse zimene mwandipatsa ine ndi makolo anga ndiponso kuti ndizichita ntchito zabwino zimene zimakukondweretsani inu. Ndilowetseni ine ku Paradiso kudzera m’chisomo chanu, kuti ndikhale pakati pa akapolo anu angwiro.”

20Iye adayendera mbalame nati, “Kodi mbalame yotchedwa mnthengu ili kuti? Kodi kapena iyo ili pamodzi ndi amene sadabwere?”

21“Ndithudi ndidzailanga iyo ndi chilango chowawa kapena ndidzaipha kupatula ngati ibweretsa kwa ine chifukwa chomveka.”

22Ndipo mbalame ya mnthengu siidachedwe ndipo idati, “Ndadziwa zimene iwe siudziwa ndipo ndikubweretsera nkhani yoona kuchokera ku Saba.”

23“Ine ndapeza munthu wamkazi akulamulira iwo ndipo iye wapatsidwa zinthu zonse zomuyenereza ndipo ali ndi Mpando waukulu wachifumu

24Ndidamupeza iye pamodzi ndi anthu ake ali kupembedza dzuwa moonjezera pa Mulungu ndipo Satana wawakongoletsera ntchito zawo zoipa ndipo wawasocheretsakunjirayoyenerandipoiwosiotsogozedwa bwino.”

25Ndi kuti sapembedza Mulungu amene amaulula zobisika za kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amadziwa zimene inu mumabisa ndi zimene mumaulula

26Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ambuye wa mpando wa Chifumu

27Solomoni adati, “Tidzaona posachedwapa ngati zimene ukunena ndi zoona kapena zabodza.”

28“Pita ukapereke kalata yangayi kwa iwo ndipo ukachoke pang’ono poyembekezera yankho lawo.”

29Mfumukazi ya ku Saba adati, “Oh inu nduna zanga! Ine ndalandira kalata yolemekezeka.”

30Kalatayi ndi yochokera kwa Solomoni ndipo ikuti, “M’dzina la Mulungu, Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.”

31“Usadzikweze kwa ine koma bwerani nonse kwa ine modzipereka.”

32Iye adati, “oh inu mafumu! Ndipatseni chilangizo chokhudza nkhani iyi ndipo sindilamula china chilichonse pokhapokha inu mutakhalapo.”

33Iwo adati, “Ife ndife olimba mtima ndiponso odziwa kumenya nkhondo molimba, ndipo nkhani ili kwa iwe. Ndipo udziwe mmene ungalamulire.”

34Iye adati, “Ndithudi mafumu akalowa mu mzinda amaononga mwaupandu ndi kuwasandutsa anthu olemekezeka kukhala onyozeka. Umo ndi mmene iwo amachitira.”

35“Koma ine ndiwatumizira mphatso ndipo ndidzaona yankho limene a Kazembe anga adzabwere nalo.”

36Ndipo pamene akazembe adadza kwa Solomoni, iye adati, “Kodi muli kundipatsa chuma chambiri? Icho chimene Mulungu wandipatsa ine ndi chabwino kuposa chuma chonse chimene wakupatsani inu. Koma inu mumasangalala ndi mphatso zanu.”

37“Bwererani kwa iwo. Ife tidzapita kwa iwo ndi magulu ankhondo amene iwo sangathe kuwagonjetsa ndipo tidzawathamangitsa m’dziko lawo mochititsa manyazi ndipo iwo adzanyozeka.”

38Iye adati, “oh inu mafumu! Kodi ndani amene angandibweretsere mpando wake wachifumu iwo asanabwerekwainemogonja?”

39Winawamphamvu, amene adalimmodziwamajiniadati,“Inendidzakubweretseraniinu musadanyamuke pa mpando wanu. Ine ndili ndi mphamvu zonyamulira mpando ndiponso ndine wokhulupirika.”

40Koma wina amene anali kudziwa Mawu a Mulungu adati “Ine ndidzakubweretserani msanga musadaphenire maso anu.” Ndipo pamene iye adaona kuti mpando wabwera kwa iye adati, “Ichi ndi chisomo cha Ambuye wanga kuti andiyese ngati ndikuthokoza kapena sindikuthokoza. Ndipo aliyense amene athokoza atero podzipezera yekha zabwino. Ndipo amene sathokoza ndithu, Ambuye wanga ali ndi zonse ndipo ndi Wolemekezeka.”

41Ndipo iye adati, “Sinthani mpando wake wachifumu kuti tione ngati iye akhoza kuuzindikira kapena ayi.”

42Ndipo pamene mfumukazi inadza kwa Solomoni idafunsidwa kuti, “Kodi mpando wako wachifumu ndi otere?” Iye adati, “Ukukhala ngati umenewu” ndipo ife tinadziwa kale ndipo tagonja kwa Mulungu mwamtendere.”

43Zinthu zimene amapembedza zoonjezera pa Mulungu ndi zimene zamusokoneza. Iye adali mmodzi wa anthu osakhulupirira

44Iye adauzidwa kuti, “Lowa mnyumba yachifumu.” Ndipo pamene iye anaiona iyo, adaganiza kuti ndi dziwe la madzi ndipo miyendo yake adaionetsa poyera. Solomoni adati, “Iyi ndi nyumba yachifumu yomatidwa ndi magalasi.” Iye adati, “Ambuye, ine ndalakwira mzimu wanga. Tsopano ndili kudzipereka pamodzi ndi Solomoni kwa Mulungu, Ambuye wazolengedwa zonse.”

45A Thamoud, ndithudi, tidawatumizira m’bale wawo Saleh, amene adati, “Muzipembedza Mulungu basi.” Koma iwo adagawikana m’magulu awiri okangana

46Iye adati, “Anthu anga! Kodi bwanji mufuna kubweretsa choipa msanga musanabweretse chabwino? Nanga ndi chifukwa chiyani simupempha chikhululukiro kwa Mulungu kuti mukhoza kupeza chisomo chake?”

47Iwo adati, “Ife tili kuona choipa chochokera kwa iwe ndiponso kwa anthu amene amakutsatira iwe.” Iye adati, “Choipa chimene muli kuchiona chili kuchokera kwa Mulungu. Inu ndinu anthu amene muli kuyesedwa.”

48M’mizinda mwawo mudali anthu asanu ndi anayi amene anali kuchita zoipa mdziko ndipo samachita zabwino ayi

49Iwo adati, “Tiyeni tonse tilumbire, dzina la Mulungu, kuti timuphe nthawi ya usiku pamodzi ndi a pabanja lake lonse. Ndipo tidzawauza abale ake kuti, “Ife kudalibe pamene iwo anali kuphedwa. Ndipo zimene tili kunena ndi zoona zokhazokha.”

50Iwo adachita chiwembu ndipo nafenso tidachita chiwembu iwo osadziwa chilichonse

51Ndipo taona zotsatira zake za chiwembu chawo. Ife tidawaonongeratu pamodzi ndi anthu awo onse

52Chifukwa chakuti iwo adalakwa, nyumba zawo zimene anali kukhalamo tsopano ndi mabwinja. Ndithudi m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira

53Ndipo Ife tidapulumutsa anthu onse okhulupirira ndipo anali kuopa Mulungu

54Loti kwa anthu ake, “Kodi inu mukuchita zinthu zochititsa manyazi pamene muli kuona?”

55“Kodi inu muli kuchita chiwerewere ndi amuna anzanu pokwaniritsa zilakolako zanu ndi kusiya akazi? Inu ndinu mbuli basi.”

56“Yankho lawo silidali lina koma kuti, “Chotsani anthu a Loti mu mzinda wanu. Awa ndi anthu amene afuna kudziyeretsa.”

57Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake kupatula mkazi wake amene adatsalira m’chilango

58Ndipo tidawalasa iwo ndi mvula ya miyala imene idagwa pa iwo. Ndi mvula yoipa imene idagwera iwo amene adachenjezedwa

59Nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu ndipo mtendere ukhale pa Atumwi ake amene Iye wawasankha. Kodi wabwino ndani Mulungu kapena mafano amene amawapembedza yoonjezera pa Mulungu?”

60Kapena wabwino ndi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukutumizirani mvula kuchokera kumwamba ndi kubweretsa minda ya chisangalalo? Iwo sangathe kumeretsa mitengo. Kodi pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Koma iwo ndi anthu amene amafanizira ena ake kukhala ofanana ndi Mulungu

61Kapena Iye amene adakhazikitsa dziko ndi kulithirira ilo ndi mitsinje ya madzi oyenda; ndipo wakhazikitsa mapiri pa dziko ndipo waika malire pakati pa nyanja ziwiri. Kodi pali mulungu wina woonjezera pa Mulungu weniweni? Koma ambiri a iwo ndi osadziwa

62Kapena Iye amene amayankha mapemphero a munthu opanikizika pamene amupempha Iye ndipo amamuchotsera mavuto. Ndiyetu amene wakupatsani dziko lapansi kuti muzikhalamo. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Ndi zazing’ono zimene mumakumbukira

63Kapena ndi Iye amene amakutsogolerani mu mdima pa mtunda kapena pa nyanja ndipo amatumiza mphepo ngati yonyamula uthenga wabwino wa chisomo chake. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Mulungu ndi wapamwamba kuposa zimene amamufanizira nazo

64Kapena Iye amene poyambirira adapanga zolengedwa ndiponso amene adzatidzutsanso kukhala ndi moyo m’moyo umene uli nkudza ndiponso amene amakupatsani chakudya kuchokera ku nthaka ndi kumwamba? Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Tionetseni chizindikiro chanu ngati zimene mukunenazi ndi zoonadi.”

65Nena, “Palibe amene ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene amadziwa zobisika kupatula Mulungu. Ndiponso anthu sadziwa nthawi imene adzaukitsidwa kukhalanso ndi moyo.”

66Kodi kuzindikira kwawo m’moyo umene uli nkudza kwakwaniritsidwa? Iwo ndi okaika pa zamoyo umene uli nkudza ndipo maso awo ndi otsekeka pa za iwo

67Anthu osakhulupirira adati, “Kodi pamene ife ndi makolo anthu, tisanduka dothi tidzaukitsidwanso?”

68“Ndithudi ife tidalonjezedwa ndiponso makolo athu. Ichi si china ayi koma nkhani zopanda pake za anthu akale.”

69Nena, “Pitani pa dziko lonse lapansi ndipo mukaone zimene zidawaonekera anthu ochimwa.”

70Usachite chisoni kapena kuvutika mu mtima chifukwa cha ziwembu zimene apanga

71Ndipo iwo amati, “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene muli kunenazi ndi zoona?”

72Nena, “Mwina gawo lina la zimene muli kufuna kuti zidze msanga zili pafupi kudza.”

73Ndipo, ndithudi, Ambuye wako ndi wokoma mtima kwa anthu, koma ambiri a iwo sathokoza ayi

74Ndipo, ndithudi, Ambuye wako amadziwa zonse zimene zimabisika m’mitima mwawo ndiponso zonse zimene amaulula

75Kulibe chinsinsi kumwamba kapena padziko lapansi chimene sichidalembedwe mu Buku lake lolemekezeka

76Buku la Korani lili kuwauza ana a Israyeli zambiri zimene iwo amatsutsana

77Ndipo limeneli ndi chenjezo ndiponso madalitso kwa anthu okhulupirira m’choonadi

78Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo ndi chiweruzo chake. Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini kudziwa za chinthu china chilichonse

79Kotero iwe ika chikhulupiriro chako mwa Mulungu chifukwa iwe uli pa choonadi chenicheni

80Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu osamva kuti amve kuitana kwako pamene iye atembenuka

81Si udindo wako kutsogolera anthu a khungu kuti aleke kusochera. Palibe munthu amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chivumbulutso chathu ndipo amadzipereka kwathunthu

82Patsiku limene chiweruzo chathu chidzayandikira kwa osakhulupirira, Ife tidzawabweretsera chinyama chimene chidzayankhula nawo kuchokera ku dziko lapansi chifukwa munthu sanakhulupirire chivumbulutso chathu

83Patsiku limeneli, tidzasonkhanitsa kuchokera ku mtundu uliwonse gululaanthuamenesadakhulupirirechivumbulutsochathu. Iwo adzasonkhanitsidwa ndi kuikidwa m’mizere

84Mpaka pamene adzafike pamalo a chiweruzo, Mulungu adzati, “Kodi inu mudakana chivumbulutso changa ngakhale kuti inu simumadziwa chilichonse cha chivumbulutsocho? Kodi ndi chiyani mumachita?”

85Chionongeko chidzadza pa iwo chifukwa cha zoipa zawo ndipo iwo adzasowa chowiringula

86Kodi iwo saona mmene tidakonzera usiku kuti ukhale mpumulo ndi masana kuti uziwapatsa kuwala? Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

87Patsikulimeneli, lipengalidzalizidwandipoonseamene amakhala kumwamba ndi padziko lapansi adzagwidwa ndi mantha kupatula okhawo amene Mulungu adzafuna kuwapatula mu zimene zi. Onse adzabwera kwa Iye modzichepetsa

88Iwe udzaona mapiri ndi kuwaganizira kuti ndi okhazikika koma iwo adzayenda ngati mmene mitambo imachitira. Uwu ndi mchitidwe wa Mulungu amene wakonza bwino lomwe chinthu chilichonse. Ndithudi Iye amadziwa bwino zonse zomwe mumachita

89Iwo amene achita zabwino adzalandira mphotho imene ili yabwino ndipo adzakhala osakhudzidwa ndi zochititsa mantha za tsiku limeneli

90Koma iwo amene achita zoipa adzaduduluzidwa pa mphumi zawo kunka ku moto. “Kodi inu simudzalandira malipiro ofanana ndi ntchito zanu?”

91Nena, “Ine ndalamulidwa kutumikira Ambuye wa mzinda uno umene waupanga kuti ukhale Woyera. Zinthu zonse ndi zake. Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi mwa odzipereka.”

92Ndipo ndalamulidwa kuwerenga Buku la Korani. Aliyense amene atsatira njira yoyenera atero podzithandiza yekha. Kwa iye amene asochera nena “Ine si ndine kanthu kena koma mmodzi wa iwo ochenjeza anthu.”

93Ndipo nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu! Iye adzakulangizani zizindikiro zake ndipo inu mudzazizindikira. Ambuye wanu saiwala zimene mumachita.”

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath