Chisilamu
kubwerera

26. Ash-Shu'araa

1Ta Sin Mim

2Awa ndi mawu omveka a Buku la Korani

3Iwe mwina ukhoza kudziononga ndi madandaulo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo

4Ngati Ife tifuna, tikhoza kuwavumbulutsira chizindikiro chochokera kumwamba chimene makosi awo adzakhota modzichepetsa

5Palibe chenjezo latsopano limene limadza kuchokera kwa Mwini chisoni chosatha koma iwo amalikana

6Ndithudi iwo amakana mawu a Mulungu koma nkhani zidzadza kwa iwo zokhudza zinthu zimene iwo amazichita chipongwe

7Kodi iwo saona nthaka, mmene ife tameretsamo mbewu zabwino zosiyanasiyana

8Ndithudi m’menemu muli chizindikiro komabe ambiri a iwo sakhulupirira ayi

9Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndiponso Mwini chisoni chosatha

10Ndipo pamene Ambuye wako adamuitana Mose adanena kuti, “Pita kwa anthu opanda chilungamo.”

11Kodi anthu a Farawo sangaope

12Iye adati, “Ambuye wanga! Ndithudi ine ndili kuopa kuti adzandikana.”

13“Ndipondikhozakupsamtimandikulepherakuyankhula. Tumizani Aroni.”

14“Ndipo iwo ali ndi mangawa ndi ine ndipo ndichita mantha kuti akhoza kukandipha.”

15Mulungu adati, “Nkosatheka kutero! Kotero pitani nonse awiri ndi zizindikiro zathu. Ife tidzakhala ndi inu ndipo tidzamva.”

16Ndipo mukakafika kwa Farawo mukamuuze kuti, “Ife ndife Atumwi ochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse.”

17“Motero alekeni ana a Israyeli kuti apite ndi ife.”

18(Farawo) adati, “Kodi ife sitidakurere iwe pamene udali wamng’ono? Ndipo iwe unakhala pakati pathu zaka zambiri.”

19“Ndipo iwe udachita chimene udachita. Ndithudi iwe ndiwe mmodzi wa anthu osathokoza.”

20(Mose) adati, “Ine ndidachita chimenecho popeza nthawi imeneyo ndidali wosadziwa china chilichonse.”

21“Motero ine ndidathawa inu nonse pa nthawi imene ndidakuopani koma tsopano Ambuye wanga wandipatsa luntha ndiponso wandipanga ine kukhala mmodzi mwa Atumwi ake.”

22“Ndipo uwu ndi mwayi umene ubwino wake iwe uli kundinyogodola. Iwe wasandutsa ana a Israyeli kukhala akapolo ako.”

23Farawo adati, “Kodi Ambuye wa zolengedwa zonse ndani?”

24(Mose) adati, “Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo ngati inu mufuna kukhulupirira.”

25(Farawo) adawafunsa anthu amene adamuzungulira! “Kodi muli kumva zimene ali kunenazi.”

26(Mose) adapitiriza kuti, “Ambuye wanu ndiponso Ambuye wa makolo anu akale.”

27(Farawo) adati, “Ndithudi Mtumwi amene watumizidwa kwa inu ndi wopenga.”

28(Mose) adati, “Iye ndi Ambuye wa kum’mawa ndi kumadzulo ndi zonse zimene zikhala kumeneko ngati muli ozindikira.”

29(Farawo) adayankha kuti, “Ngati iwe utumikira mulungu wina kupatula ine, ndithudi ndikupanga kukhala mmodzi wa anthu okhala ku ndende.”

30(Mose) adafunsa kuti, “Kodi zingakhale choncho ngakhale nditakulangiza chizindikiro choonekeratu? “

31(Farawo) adati, “Tilangize chizindikiro chako ngati zonse zimene unena ndi zoona.”

32Motero Mose adaponya ndodo yake pansi ndipo nthawi yomweyo idasanduka njoka yeniyeni

33Ndipo Iye adatulutsa dzanja lake ndipo nthawi yomweyo lidasanduka loyera kwa iwo amene adaliona

34Farawo adauza nduna zake kuti, “Ndithudi munthu uyu ndi wodziwa matsenga.”

35“Iyeyu afuna kukuchotsani m’dziko lanu ndi matsenga ake. Kodi ulangizi wanu ndi wotani ndipo ukupereka langizo lanji?”

36Iwo adati, “Muyambe mwawasunga iye pamodzi ndi m’bale wake kwa kanthawi kochepa. Tumizani mithenga ku mizinda yanu

37Abweretse kwa inu munthu aliyense yemwe ndi wodziwa matsenga kwambiri.”

38Motero anthu amatsengawa adasonkhanitsidwa patsiku lodziwika lomwe adagwirizana

39Ndipo anthu adafunsidwa kuti, “Kodi nonse mudzasonkhana?”

40“Kuti mwina ife tikhoza kudzatsatira a matsenga ngati iwo atapambana.”

41Ndipo pamene anthu onse amatsenga adadza kwa Farawo, iwo adati kwa Farawo, “Kodi mudzatilipira ngati titapambana?”

42Iye adati, “Inde. Ndipo ndithudi inu mudzakhala kufupi ndi Ine.”

43Mose adawauza kuti, “Ponyani pansi chilichonse chimene mufuna kuponya.”

44Ndipo iwo adaponya zingwe ndi ndodo zawo ndipo adati: “Mwa mphamvu ya Farawo, ndithudi, ife tipambana.”

45Ndipo Mose adaponya ndodo yake ndipo nthawi yomweyo idameza zonse zabodza zimene iwo adapanga

46Ndipo anthu amatsenga onse aja adagwa pansi mogwada

47Iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa zolengedwa zonse.”

48“Ambuye wa Mose ndi Aroni”

49Farawo adati, “Kodi inu mwakhulupirira mwa iye pamene ine sindinakupatseni chilolezo? Ndithudi iye ndi mtsogoleri wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi posachedwapa mudzazindikira. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu moisiyanitsa. Ndidzakudulani dzanja lamanja ndi mwendo wamanzere ndiponso ndidzakupachikani pa mtanda.”

50Iwo adati, “Zilibe kanthu chifukwa ndithudi ife tidzabwerera kwa Ambuye wathu.”

51“Ndithudi Ife tili ndi chiyembekezo kuti Ambuye wathu adzatikhululukira machimo athu popeza ndife oyamba kukhulupirira.”

52Ndipo tidamulamula Mose kuti, “Nyamuka nthawi ya usiku ndi akapolo anga chifukwa, ndithudi, inu mulondoledwa ndi gulu la adani anu.”

53Ndipo Farawo adatumiza mithenga ku mizinda yonse

54“Ndithudi anthu amenewa ndi kagulu ka anthu ochepa.”

55“Ndithudi anthu amenewa atipsetsa mtima.”

56“Ife tonse tili tcheru.”

57Ndipo tidawachotsa m’minda ndi mu a kasupe

58Ndiponso m’chuma ndi m’malo alionse olemekezeka

59Kotero tidawapanga ana a Israyeli kukhala alowa m’malo a zinthu za anthu a Farawo

60Pamene dzuwa linali kutuluka, iwo adalondoledwa ndi adani awo

61Ndipo pamene magulu awiriwa adaonana wina ndi mnzake, anthu a Mose adati, “Ndithudi atipeza.”

62Mose adati, “Iyayi. Ndithudi Ambuye wanga ali ndi ine ndipo adzanditsogolera.”

63Ndipo tidalamulira Mose kuti, “Menya madzi a m’nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo nyanja idagawanika pakati, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu

64Ndipo anthu a Farawo tidawayandikitsa ndi nyanja ija

65Ndipo Ife tidapulumutsa Mose ndi onse amene adali ndi iye

66Ndipo tidamiza ena

67Ndithudi mu ichi muli phunziro komabe anthu ambiri sakhulupirira ayi

68Ndithudi Ambuye wako! Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha

69Ndipo afotokozere nkhani za Abrahamu

70Pamenepo iye adanena kwa abambo ake ndiponso kwa anthu ake kuti, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?”

71Iwo adati, “Timatumikira mafano ndipo timapempha kwa iwo modzipereka kwambiri.”

72Ndipo adati, “Kodi iwo amakumvani pamene mumawapempha?”

73“Kodi amakuthandizani kapena kukuonongani?”

74Iwo adati, “Iyayi. Koma ife tidawapeza makolo athu akupembedza mafano.”

75Iye adati, “Kodi inu muli kuzidziwa zimene muli kuzipembedza?”

76“Inu ndiponso makolo anu akale?”

77“Ndithudi onse ndi adani anga kupatula Ambuye wachilengedwe.”

78“Amene adandipanga ine ndipo ndiye amene amandipatsa chilangizo.”

79“Ndipo ndiye amene amandipatsa chakudya ndi chakumwa.”

80“Ndipo ndikadwala, ndi Iye amene amandichiza.”

81“Ndipo ndiye amene adzandipangitsa kuti ndife ndi kudzandibwezeranso moyo.”

82“Ndi amene ine ndimayembekezera kuti adzandikhululukira machimo anga pa tsiku lachiweruzo”

83Ambuye ndipatseni luntha ndipo mundilole kuti ndikhale pakati pa anthu ochita zabwino

84Ndipatseni ulemerero umene udzatchulidwe ndi mibadwo yomwe ikubwera mtsogolo

85Ndipo ndiikeni m’gulu la anthu amene adzakhala kumalo a mtendere a ku Paradiso

86Akhululukireni abambo anga ndithudi iwo ali mmodzi mwa anthu osochera

87Musadzandichititse manyazi patsiku limene anthu adzaukitsidwa kwa akufa

88Tsiku limene chuma ndi ana sizidzathandiza wina aliyense

89Kupatula yekhayo amene adzadza kwa Mulungu ndi mtima woyera

90Pamenepo Paradiso idzayandikiritsidwa kwa anthu angwiro

91Ndipo Gahena idzaonetsedwa poyera kwa anthu ochimwa

92Mawu adzanenedwa kwa iwo kuti, “Kodi mafano anu aja amene mumatumikira ali kuti?”

93Kuwonjezera pa Mulungu weniweni? Kodi iwo akhoza kukuthandizani inu kapena kudzithandiza okha?”

94Ndipo iwo ndi onse ochimwa adzaponyedwa ku Gahena

95Ndiponso pamodzi ndi magulu onse a Satana

96Iwo adzati pamene adzakhala ali kukangana kumeneko

97“Pali Mulungu, ndithudi, ife tidali ochimwa moonekeratu.”

98Pamene tidakusandutsani inu kukhala ofanana ndi Ambuye wa zolengedwa zonse

99Palibe ena koma anthu ochita zoipa amene adatisocheretsa ife

100Palibe wina woti angatipepesere ife

101Ndiponso palibe bwenzi lenileni

102Koma tikadakhalanso ndi moyo, tikadakhala anthu okhulupirira

103Ndithudi mu zimenezi muli chizindikiro koma anthu ambiri sakhulupirira ayi

104Ndithudi Ambuye wanu! Ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha

105Anthu a m’badwo wa Nowa adakana Atumwi awo

106Pamene Nowa adati, “Kodi inu simungaope Mulungu ndi kumumvera Iye?”

107“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.”

108“Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”

109“Ine sindikupemphani malipiro ena alionse chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire ine kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”

110“Kotero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”

111Iwo adati, “Kodi ife tikukhulupirire iwe pamene anthu onyozeka ndiwo amene amakutsatira iwe?”

112Nowa adati, “Kodi ine ndikudziwa chiyani za chimene iwo amachita?”

113“Ambuye wanga ndiye amene akhoza kuweruza ngati mumazindikira.”

114“Ndipo ine sindidzathamangitsa anthu okhulupirira moona.”

115“Ine ndine wopereka chenjezo poyera.”

116Iwo adati, “Iwe Nowa; ngati siusiya zimene uchita udzaponyedwa miyala.”

117Iye adati, “Ambuye wanga! Ndithudi anthu anga akundikana.”

118Motero weruzani mwachilungamo pakati pa ine ndi iwo. Ndipulumutseni ine pamodzi ndi anthu okhulupirira amene ali ndi ine

119Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo

120Ndipo pambuyo pake tidamiza ena onse ndi chigumula

121Ndithudi mu chimenechi muli phunziro komabe ambiri sakhulupirira

122Ndithudi Ambuye wako ndi Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha

123Anthu a ku Aad sanakhulupirire Atumwi awo

124Pamene m’bale wawo Houd adati, “Kodi inu simungakhale ndi mantha ndi Mulungu?”

125“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.”

126“opani Mulungu ndipo munditsate ine.”

127“Pa ntchito iyi, ine sindipempha malipiro kuchokera kwa inu chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”

128“Kodi inu mukumamanga nyumba pamalo paliponse pokwera mofuna kudzisangalatsa?”

129“Kodi muli kumanga nyumba zokongola ndi zolimba ngati kuti mudzakhalamo mpaka kalekale?”

130“Ndipo pamene mumenya anthu mumamenya ngati anthu ankhanza.”

131“Motero opani Mulungu, ndipo mundimvere ine.”

132“Ndipo muopeni Iye amene wakupatsani inu zinthu zonse zimene mumazidziwa.”

133“Iye wakupatsani nyama ndi ana,”

134“Ndiponso minda ndi a kasupe;”

135“Ndithudi ine ndili kuchita mantha ndi chilango chimene chidzadza pa inu pa tsiku loopsa.”

136Iwo adati, “Ndi chimodzimodzi kwa ife kaya utilalikira kapena ayi.”

137“Zonse zimene uli kutiopseza nazo ndi chikhalidwe cha anthu amakedzana.”

138“Ife sitidzalangidwa ayi.”

139Iwo adamukana iye ndipo Ife tidawaononga onse. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro koma ambiri sakhulupirira ayi

140Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha

141Anthu a Thamoud adakana Atumwi awo

142Pamene m’bale wawo Saleh adati, “Kodi inu simungakhale ndi mantha ndi Mulungu?”

143“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu okhulupirika.”

144“Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”

145“Pa ntchito iyi ine sindili kukupemphani malipiro. Palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”

146“Kodi inu muganiza kuti mudzasiyidwa mu mtendere wa m’dziko lino?”

147“M’kati mwa minda ndi a kasupe.”

148“Minda ya chimanga ndi mitengo ya tende imene yapatsa zipatso zambiri.”

149“Ndipo muboola mapiri ndi kumangamo nyumba zanu mwaukatswiri;”

150“Khalani ndi mantha ndi Mulungu ndipo mundimvere ine.”

151“Musamvere malamulo a anthu oononga.”

152“Amene amachita zoipa padziko lapansi ndipo sakonza makhalidwe awo.”

153Iwo adati, “Iwe uli mmodzi mwa olodzedwa.”

154“Iwe ndiwe munthu wonga ife tomwe. Tilangize chizindikiro ngati zimene ukunenazi ndi zoona”

155Iye adati, “Iyi ndi ngamira yaikazi. Iyo idzamwa madzi patsiku lake ndipo inu mudzamwa patsiku lanu lokhazikitsidwa.”

156“Musaizunze ayi chifukwa mukatero chilango cha tsiku loopsa chidzadza kwa inu.”

157Komabe iwo adaipha iyo ndipo adanong’oneza bombono

158Chilango chidawapeza iwo. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro koma ambiri a iwo sakhulupirira

159Ndithudi Ambuye wako! Indedi ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha

160Anthu a Loti adakana Atumwi awo

161Pamene m’bale wawo Loti adati, “Kodi inu simungaope Mulungu?”

162“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.”

163“Opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”

164“Ine sindili kupempha kuti mundilipire chifukwa cha ichi ayi chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”

165“Kodi inu mwasankha kuti muzigonana ndi amuna anzanu mwa zolengedwa zonse

166“Kusiya akazi amene Mulungu adakulengerani? Koma inu ndinu anthu olakwa kwambiri.”

167Iwo adati, “Iwe Loti! Ngati siusiya zimenezi ndithudi udzakhala mmodzi mwa othamangitsidwa.”

168Iye adati, “Ine ndili kudana ndi makhalidwe anu.”

169“Ambuye wanga! Ndipulumutseni ine pamodzi ndi a pabanja langa ku ntchito zawo zoipa.”

170Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake onse

171Kupatula mayi wokalamba, pakati pa amene adatsalira m’mbuyo

172Ndipo Ife tidawaononga kwambiri ena onse

173Ndipo choipa chidali chilango cha mvula imene idagwa pa iwo amene adachenjezedwa koma sadamvere

174Ndithudi mu ichi muli phunziro koma ambiri a iwo sakhulupirira

175Ndithudi Ambuye wako ndiye mwini mphamvu zonse ndi mwini chisoni chosatha

176Nawonso anthu okhala m’nkhalango adakana Atumwi

177Pamene Shaibu adawauza kuti, “Kodi inu simungaope Mulungu?”

178“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirira.”

179“Opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”

180“Ine sindikupemphani malipiro chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”

181“Perekani muyeso oyenera ndipo musachepetse.”

182“Yesani ndi miyeso yabwino.”

183“Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo kapena kulowetsa chisokonezo m’dziko.”

184“Muopeni Iye amene adakulengani inu ndi mibadwo yakale.”

185Iwo adati, “Ndithudi iwe walodzedwa.”

186“Iwe ndiwe munthu wolingana ndi ife. Ndithudi ife tili kuganiza kuti iwe uli kunama.”

187“Tigwetsere mtambo kuchokera kumwamba ngati zimene uli kunena ndi zoonadi.”

188Iye adati, “Ambuye wanga amadziwa kwambiri chimene inu mumachita.”

189Iwo adamukana iye kotero chilango cha thambo ndi moto chidawaononga. Ichi chidali chilango cha tsiku loopsa

190Ndithudi mu chimenechi muli chiphunzitso koma ambiri a iwo sakhulupirira

191Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha

192Buku lolemekezekali lavumbulutsidwa ndi Ambuye wa zolengedwa zonse

193Mzimu wokhulupirika udabweretsa Bukuli

194Ku mtima wako kuti ukhoza kuchenjeza mitundu ya anthu

195Mu chinenero chomveka cha Chiarabu

196Ndithudi lili kupezeka mu mawu a Mulungu akale

197Kodi si chizindikiro kwa iwo kuti anthu ophunzira a ana a Israyeli amalidziwa

198Ngati Ife tikadaivumbulutsa kwa munthu wa mtundu wina uliwonse yemwesi wa Chiarabu

199Kuti iye ailakatule kwa iwo ndipo sakadakhulupirira iwo mwa Bukulo

200Kotero Ife tidaipanga iyo kuti ilowe m’mitima ya anthu ochitazoipa

201Iwosadzakhulupiriramuilompakapamene adzaona chilango chowawa

202Ndipo icho chidzadza kwa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sakudziwa

203Ndipo iwo adzati, “Kodi ife sitidzapatsidwanso nthawi?”

204Kodi iwo angafune kuti chilango chathu chidze msanga

205Tandiuza. Ngati Ife titawalola kukhala mu mtendere wa zaka zambiri

206Ndipo pambuyo pake chilango chimene chidalonjezedwa chidza pa iwo

207Chisangalalo chawo chimene adapatsidwa chidzakhala chopanda phindu

208Palibe mtundu wa anthu umene tidaonongapo kale umene sitidautumizire owachenjeza

209Monga chenjezo ndipo Ife si ndife opondereza ayi

210Si a Satana amene adabweretsa Korani ino ayi

211Si koyenera kwa iwo ndiponso sangathe kutero

212Ndithudi iwo amanidwa kumva za Bukuli

213Musapembedze milungu ina kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa mukatero mudzakhala m’gulu limene lidzalangidwa

214Achenjeze abale ako amene ali pafupi ndi iwe

215Ndipo onetsa chifundo kwa anthu okhulupirira amene amakutsatira iwe

216Ngati iwo sakumvera iwe, unene kuti, “Ine sindidzaimbidwa mlandu chifukwa cha zimene mumachita.”

217Ika chikhulupiriro chako mwa Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha

218Amene amakuona pamene umaimirira popemphera

219Ndi machitidwe ako pakati pa anthu opemphera

220Mulungu amamva chilichonse ndipo amadziwa china chilichonse

221Kodi ndi kuuzeni za munthu amene Satana amamutsikira

222Iwo amadza pa munthu wabodza ndi wochimwa

223Iwo amamvera mabodza okhaokha ndipo komaambiriaiwondiabodza

224Alakatuliamatsatidwandi anthu ochita zoipa

225Kodi simuona kuti iwo amangonena nkhani iliyonse mu zolakatula zawo

226Ndipo iwo amakamba zinthu zimene iwo sachita

227Kupatula okhawo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndi kumakumbukira Mulungu kwambiri ndi kudziteteza pambuyo pa kuponderezedwa. Ndipo iwo amene amachita zoipa adzadziwa chimene chidzawagadabuza

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath