25. Al-Furqaan
1Alemekezeke Iye amene adavumbulutsa Korani kwa Mtumwi wake kuti akhoza kuchenjeza mitundu ya anthu
2Iye ndiye Mfumu ya kumwamba ndi dziko lapansi. Iye ndiye amene sadabereke mwana ndipo alibe wothandizana naye mu Ufumu wake. Iye ndiye amene adalenga zinthu zonse ndipo adakhazikitsa mmene zili ndi mapeto ake
3Komabe anthu osakhulupirira amapembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni imene siingathe kulenga china chilichonse chifukwa chakuti nayonso idachita kulengedwa. Ndi imene singathe kuwathandiza kapena kuwaononga ndiponso imene ilibe mphamvu pa nkhani zokhudza imfa kapena moyo kapena kuukitsa anthu akufa
4Anthu osakhulupirira amanena kuti, “Zonsezi ndi zinthu zabodza zimene wapeka yekha, ndiponso anthu ena amamuthandiza. Zonse zimene watulutsa ndi zopanda pake ndipo zabodza
5Ndipo iwo amati, “Izi ndi nkhani zopanda pake za anthu amakedzana zimene iye walemba. Izo zimalembetsedwa kwa Iye m’mawa ndi masana aliwonse.”
6Nena, “Wavumbulutsa ndiye amene amadziwa zinsinsi za kumwamba ndi za padziko lapansi. Iye amakhululukira ndipo ndi Mwini chisoni chosatha.”
7Iwo amanena kuti, “Uyu, ndi Mtumwi wotani amene amadya ndipo amayendayenda ku msika? Kodi bwanji mngelo sanathe kutumizidwa pansi pamodzi ndi iye kudzatichenjeza ife?”
8“Nanga ndi chifukwa chiyani sadapatsidwe chuma ndipo alibe munda woti azipezako chakudya?” Ndipo anthu ochita zoipa amati, “Ndithudi munthu amene muli kumutsatira ndi wolodzedwa.”
9Taona mafanizo amene amakupatsa iwe! Iwo asochera ndipo sangathe kubwerera kunjira yoyenera
10Alemekezeke Iye amene, ngati afuna akhoza kukupatsa iwe zinthu zabwino kuposa zimenezi monga minda yothiriridwa ndi madzi a m’mitsinje ndi nyumba zachifumu
11Iyayi. Iwo amakana ola lachiweruzo, ndipo iwo amene amakana olali, Ife tawakonzera moto woyaka
12Pamene idzawaona iwo kuchokera kutali, iwo adzamva mkokomo wake
13Ndipo onse akadzamangidwa limodzi, adzaponyedwa kumalo opanikizika. Ndithudi iwo adzafuna imfa itadza pa iwo
14Lero musaitane imfa imodzi yokha ayi koma itanani imfa zambiri
15Nena, “Kodi chimenecho ndi chabwino kapena Paradiso yosatha imene anthu angwiro adalonjezedwa?” Imeneyo ndiyo mphotho yawo ndi kobwerera kwawo
16Iwo adzapeza m’menemo zonse zimene anali kufuna ndi kukhala momwemo. Limenelo ndilo lonjezo limene ndi lofunika kumapempha pafupipafupi kuchokera kwa Ambuye wako
17Patsiku limene Iye adzawasonkhanitsa onse ndi zomwe amapembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo Iye adzati, “Kodi ndinu amene munasocheza akapolo anga kapena ndi iwo okha anasochera ku njira yoyenera?”
18Iwo adzati, “Ulemerero ukhale kwa Inu! Si koyenera kwa ife kuti tisankhe otisamalira ena oonjezera pa Inu. Koma Inu mudawapatsa iwo ndi makolo awo zinthu zokoma za dziko, kotero kuti iwo adaiwala chenjezo lanu ndipo adali anthu oonongeka.”
19Kotero iwo adatsutsa mawu anu ndipo inu simungathe kuthawa kapena kupeza chithandizo ndipo aliyense amene ndi wosalungama pakati panu, Ife tidzamupatsa chilango chachikulu
20Ife sitidatumizepo Atumwi kale amene sanali kudya ndi kuyenda m’misika. Ife tidakupangani ena a inu kukhala mayesero a ena. Kodi simungapirire? Ambuye wanu amaona chilichonse
21Iwo amene alibe chikhulupiriro choti adzakumana ndi Ife amati, “Kodi ndi chifukwa chiyani angelo sadatumizidwe kwa ife? Kapena ndi chifukwa chiyani kuti ife sitingaone Ambuye wathu?” Ndithudi iwo adadzikweza kwambiri
22Patsiku limene iwo adzaona angelo, anthu ochita zoipa sadzasangalala ayi ndipo iwo adzati, “Ambuye wathu! Ikani malire pakati pa ife ndi iwo.”
23Ndipo Ife tidzabweretsa zonse zimene adachita ndikuzionetsa kuti ndi zinthu zopanda ntchito ngati fumbi louluka
24Anthu okhala ku Paradiso, adzakhala kumalo abwino patsiku limeneli ndiponso malo abwino opumulako
25Patsiku limeneli kumwamba pamodzi ndi mitambo yake idzagawanika pakati ndipo angelo adzatumizidwa pansi pano m’maudindo awo
26Patsiku limeneli ufumu wonse udzakhala wa Mwini chisoni chosatha. Limeneli lidzakhala tsiku lovuta kwambiri kwa anthu osakhulupirira
27Patsiku limeneli munthu ochita zoipa adzanong’oneza bombono nati, “Oh zikadakhala bwino ndikadakhala kuti ndidatsatira zimene Mtumwi anali kunena!”
28“oh kalanga ine! Ndikadakhala kuti sindidasankhe a uje ndi a uje kuti akhale anzanga!”
29“Mosakayika ndiwo amene adandisokoneza ine kuti ndisakhulupirire machenjezo a Mulungu pamene machenjezowo atandifika. Ndithudi Satana ndi wachinyengo nthawi zonse kwa munthu.”
30Mtumwi adati, “Ambuye wanga! Ndithudi anthu anga alikana Buku la Korani.”
31Motero Ife tapanga kwa Mtumwi aliyense mdani kuchokera kwa anthu ochimwa, anthu otsutsana naye, ndipo Ambuye wako ali wokwana kukhala wokutsogolera mu zabwino ndiponso ngati wokuthandiza wako
32Anthu osakhulupirira anati, “Kodi ndi chifukwa chiyani Korani yonse siidavumbulutsidwe kwa iye nthawi imodzi?” Ife talivumbulutsa kotero kuti tikhoza kulimbikitsa mtima wako ndipo takupatsa ilo kwa iwe mu chivumbulutso chapang’onopang’ono
33Iwo sadzatha kubwera ndi mtsutso umene Ife sitidakonze yankho loona ndi kafotokozedwe kake
34Iwo adzaduduluzidwa cha mphumi kupita ku Gahena ndipo iwo adzakhala ndi malo oipa okhalamo ndipo njira yawo ndi yosochera
35Ndithudi Ife tidavumbulutsa mawu a Mulungu kwa Mose ndipo tidamupatsa m’bale wake Aroni kuti akhale nduna yomuthandiza
36Tidawauza iwo kuti, “Pitani nonse kwa anthu amene adakana zizindikiro zathu” ndipo pambuyo pake tidawaononga kotheratu
37Akakhala anthu a Nowa, tidawamiza pamene iwo adakana Atumwi awo ndipo tidawapanga iwo kukhala phunziro kwa anthu a mitundu yonse. Ndipo anthu ochimwa tawakonzera chilango chowawa
38Mitundu ya anthu a ku Thamoud ndi Aad nawonso tidawaononga ndiponso iwo amene anali kukhala ku Raas ndi mibadwo yochuluka imene idadza pakati pawo
39Ndipo onsewa, tidawapatsa zitsanzo ndipo onse tidawaononga kotheratu
40Ndithudi anthu osakhulupirira adadutsa pa mzinda umene udaonongeka ndi madzi a mvula. Kodi iwo sadauone mzindawu? Komabe iwo adalibe chikhulupiriro mu kuukanso kwa akufa
41Nthawi zonse akakuona iwe amakunyoza ndipo amati, “Kodi uyu ndiye munthu amene akuti Mulungu wamutumiza ngati Mtumwi wake?”
42Ngati ife tikadapanda kulimba popembedza milungu yathu ndithudi iye akadatitembenuza ife kuti tisiye milungu yathu. Koma posakhalitsa iwo adzaona chilango ndipo adzadziwa kuti ndani amene adasochera kwambiri
43Kodi wamuona iye amene amayesa zilakolako zake ngati milungu? Kodi iwe ungakhale munthu wosamalira munthu wotere
44Kodi iwe umaganiza kuti ambiri a iwo angathe kumva kapena kuzindikira? Iwo si chinthu china chilichonse koma ali ngati nyama yosochera kwambiri
45Kodi iwe siuona mmeneAmbuye wako amatambasulira mthunzi? Mulungu akadafuna, akadaupanga kuti ukhale wokhazikika. Ndipo Ife tapanga dzuwa kukhala chizindikiro chake
46Ndipo timaubweretsa kwa Ife mwapang’onopang’onomosavuta
47Ndiyeamenewapanga usiku kukhala chofunda ndi tulo kuti tikhale mpumulo, ndipo wapanga usana kuti uzikhala nthawi yodzuka ndi kumagwira ntchito
48Ndiye amene amatumiza mphepo ngati mthenga wobweretsa chisomo chake ndipo timatumiza madzi abwino kuchokera kumwamba
49Ndi cholinga choti tipereke moyo ku nthaka imene inali yakufa ndi kuti timwetse zinthu zimene talenga, nyama ndi anthu ambiri
50Ndithudi tawatumizira pakati pawo, kuti akhoza kukumbukira, chisomo cha Mulungu koma anthu ambiri amakana. Ndipo iwo amasankha kusakhulupirira
51Chikadakhala chifuniro chathu, tikadautsa wowachenjeza ku mzinda uliwonse
52Iwe usawamvere anthu osakhulupirira koma limbana nawo kwambiri pogwiritsa ntchito Korani ino
53Ndiye amene adatumiza nyanja ziwiri, ina yamadzi ozuna ndi abwino pamene ina ndi yamadzi a mchere ndi owawa ndipo adakhazikitsa malire olimba kwambiri pakati pa nyanjazi
54Ndiye amene adamulenga munthu kuchokera ku madzi ndipo adamupatsa abale chifukwa cha magazi amodzi ndiponso chifukwa cha ukwati. Ndipo Ambuye wako ndiye mwini mphamvu zonse ndipo amachita zimene afuna
55Komabe anthu osakhulupirira amapembedza mafano moonjezerapa Mulungu Mafanowosangathekuwathandiza kapena kuwaononga. Munthu wosakhulupirira amathandiza Satana kuchita zoipa zosakomera Ambuye wake
56Ndipo takutumiza iwe ngati wobweretsa nkhani yabwino ndiponso munthu wopereka chenjezo
57Nena, “Ine sindili kukupemphani malipiro pa ntchito iyi ayi kupatula kuti iye amene afuna atsatire njira yoyenera yopita kwa Ambuye wake.”
58Ndipo ika chikhulupiriro chako mwa Iye wa moyo amene sakufa ayi. Ndipo mulemekeze nthawi zonse. Iye ndi okwana chifukwa Iye amadziwa bwinobwino za machimo a akapolo ake
59Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero adabuka pa chimpando chaufumu, Mwini Chisononi chosatha. Motero mufunse Iye chifukwa amadziwa china chili chonse
60Pamene zimanenedwa kwa iwo kuti, “Lambirani Mwini chisoni chosatha,” Iwo amati; “Kodi Mwini chisoni chosatha ndani? Kodi iwe ufuna kuti ife tizipembedza chilichonse chimene iwe utilamula?” Mawu amenewa amaonjezera kukana kwawo
61Alemekezeke Iye amene adalenga gulu la nyenyezi kumtambo ndipo adalenga dzuwa ndi mwezi wowala
62Ndipo ndiye amene amasinthanitsa usiku ndi usana chifukwa cha iye amene afuna kukumbukira kapena afuna kuonetsa kuyamika kwake
63Ndipo akapolo a Mwini Chisoni Chosatha ndi iwo amene amayenda modzichepetsa padziko lapansi ndipo ngati mbuli zikawayankhula mwachipongwe iwo amayankha mwaulemu
64Ndipo iwo amene amachezera pamaso pa Ambuye wawo, amagwada ndi kuima
65Amene amanena kuti, “Ambuye wathu! Tichotsereni chilango cha ku Gahena.” Ndithudi chilango chake ndi chosatha
66Ndithudi kumeneko ndi malo wonyansa kupumirako ndiponso malo wonyansa kukhalako
67Iwo akamapereka saononga chuma chawo moposa muyeso ndipo saumira koma amakhala pakatikati
68Ndipo anthu amene sapembedza mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo sakupha mzimu umene Mulungu waletsa kupatula mu njira yachilungamo ndipo sachita chigololo. Ndipo aliyense amene achita izi adzalandira chilango
69Chilango chake chidzaonjezedwa kawiri patsiku la kuuka kwa akufa ndipo adzakhala ndi manyazi nthawi zonse
70Kupatula okhawo amene alapa ndi kukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, chifukwa potero Mulungu adzasintha zoipa zawo kukhala ntchito zabwino. Ndipo Mulungu amakhululukira ndi wachisoni chosatha
71Iye amene alapa ndi kuchita ntchito zabwino, ndithudi, ndiye kuti wabwerera kwa Mulungu
72Iwo amene sapereka umboni ku zinthu zabodza ndipo akamadutsa pamalo pamene pakuchitika zinthu zoipa kapena zoletsedwa, iwo amadutsa modzilemekeza
73Amene sanyozera chivumbulutso cha Ambuye wawo ndipo pamene akumbutsidwa za icho sachita ngati kuti iwo ndi a gonthi kapena a khungu
74Ndipo anthu amene amanena kuti, “Ambuye wathu! Tipatseni chisangalalo mu akazi ndi ana athu ndipo tipangeni ife kukhala atsogoleri a iwo amene amakuopani Inu!”
75Amenewa adzalipidwa Paradiso wa pamwamba chifukwa cha kupirira kwawo. Kumeneko adzalandiridwa ndi malonje abwino mawu amtendere ndi aulemu
76Adzakhala kumeneko nthawi zonse ndipo ndi malo abwino kukhalako ndiponso ndi malo abwino opumirako
77Nena “Ambuye wanga amakusamalani inu chifukwa cha mapempheroanuakwa Iyeyekha. Komatsopano, ndithudi, inu mwamukana Iye. Motero chilango chidzakhala chanu mpaka kalekale.”
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath