Chisilamu
kubwerera

23. Al-Muminoon

1Anthu okhulupirira ndiwo opambana

2Iwo amene amadzichepetsa akamapemphera

3Ndi iwo amene amalewa nkhani zabodza

4Ndipo amapereka zaulere kwa anthu osauka

5Ndi iwo amene amadziteteza ku chiwerewere

6Kupatula kwa akazi awo kapena akapolo awo akazi, chifukwa iwo sangadzudzulidwe

7Koma amene angafune zina pamwamba pa zimene tawaloleza anthu otere ndi ochimwa

8Amene amakwaniritsa malonjezo ndi mapangano awo

9Ndi iwo amene amasunga mapemphero awo

10Amenewa ndithudi ndiwo amene adzalowa

11Iwo adzalowa ku Paradiso ya pamwamba ndipo adzakhalamo mpaka kalekale

12Ndithudi Ife tidapanga munthu kuchokera ku dothi labwino

13Titatero tidamukonza iye kukhala dontho la umuna m’malo otetezedwa mu msana

14dontho la umunali tidalipanga kukhala dontho la magazi ndipo dontho lamagazili tidalipanga kukhala m’bulu wa mnofu. Ndipo mnofu umenewu tidaukonza kukhala mafupa ndipo tidakuta mafupa ndi mnofu. Kotero tidamupanga iye kukhala chilengedwe china. odalitsa akhale Mulungu, Namalenga wabwino kwambiri mwa onse

15Ndipo pambuyo pake inu nonse mudzafa

16Ndipo mudzapatsidwanso moyo patsiku la kuuka kwa akufa

17Ife tidalenga miyamba isanu ndi iwiri pamwamba panu ndipo kwa zolengedwa zathu. Ndipo Ife sitikhala osalabadira ayi

18Ife timatumiza madzi kuchokera kumwamba m’muyeso wokwana ndipo timawalowetsa pansi pa nthaka. Ndipo Ife tili ndi mphamvu yowachotsa madziwo

19Ndipo Ife timakutulutsirani mmenemo minda ya tende ndi mphesa, m’mene muli zipatso zanu zambiri zimene zina mwa izo mumadya

20Mtengo umene umamera pa phiri la Sinai, umapereka mafuta ndiponso ndiwo kwa anthu

21M’nyama namonso muli chizindikiro choonetsa mphamvu zathu. Inu timakumwetsani zimene zili m’mimba mwake ndipo mumadya nyama yake ndiponso mumapeza phindu lambiri

22Ndipo pa izo ndi m’zombo zimene zimayenda pa nyanja, inu mumanyamulidwa

23Tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo iye adati, “Tumikirani Mulungu anthu anga chifukwa mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Iye?”

24Akuluakulu osakhulupirira a anthu ake adati, “Munthu uyu ndi wolingana ndi inu, iye ali kungodziyenereza kuti ndi wopambana pakati panu.” Mulungu akadafuna, akadatumiza angelo. Ndiponso zinthu za mtundu uwu sitidamvepo kuchokera kwa makolo athu akalekale

25Ndithudi ameneyu ndi wopenga, ndipo mumuyang’anire pa kanthawi.”

26Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kundikana.”

27Ife tidavumbulutsa chifuniro chathu kwa iye ponena kuti, “Khoma chombo chimene Ife tidzayang’anira molingana ndi chilangizo chathu. Pamene chiweruzo chathu chidza ndipo madzi asefukira kuchokera ku ng’anjo, utenge zolengedwa ziwiriziwiri, zazimuna ndi zazikazi ndiponso kuchokera kwa iwo a m’nyumba mwako kupatula okhawo amene adanenedwa kuti adzaonongeka. Usandipemphe kuti ndipulumutse iwo amene adachita zoipa chifukwa iwo adzamizidwa.”

28Ndipo pamene iwe ndi iwo amene akutsata iwe mulowa m’chombo, nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu amene watipulumutsa ife kuchoka ku mtundu wa anthu oipa.”

29Ndipo nena: “Ambuye wanga! Ndithandizeni kuti ndikafike pamalo podalitsika chifukwa Inu ndinu wabwino wa onse amene amafikitsa pamalo okocheza.”

30Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro zooneka. Ndithudi Ife timawaika anthu m’mayesero

31Potero Ife tidapanga mtundu wa anthu a tsopano pambuyo pawo

32Ndipo tidatumiza kwa iwo Mtumwi wa mtundu wawo amene adati, “Tumikirani Mulungu chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Mulungu?”

33Koma akuluakulu a anthu osakhulupirira a anthu ake, amene adakana za moyo umene uli nkudza ndi amene tidawapatsa zinthu zabwino za m’moyo uno adati, “Munthu uyu ndi munthu monga inu nomwe amene akudya zimene mumadya inu ndi kumwa zimene inu mumamwa.”

34“Ngati inu mumvera munthu wonga inu nomwe, ndithudi, inu mudzatayika.”

35“Kodi iye ali kukuopsezani kuti pamene inu mutafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa mudzadzuka ndi kukhalanso ndi moyo?”

36“Zimene inu muli kuopsezedwa nazo zili kutali.”

37“Kulibenso moyo wina koma moyo wathu wapadziko lapansi basi. Ife timafa ndi kukhala ndi moyo ndipo ife sitidzadzukanso ayi.”

38“Munthu uyu ndi odziyenereza amene ali kunena za Mulungu zimene sizili zoona ayi. Ife sitidzamukhulupirira.”

39Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kunditsutsa.”

40Iye adati, “Posachedwapa iwo adzanong’oneza bombono.”

41Chilango chathu chidawapeza mwachilungamo ndipo tidawafafaniza monga zinyalala. Chionongeko kwa anthu onse ochimwa

42Atapita awa tidalenganso mitundu ina ya anthu

43Palibeanthuameneangafulumizitsekapenakuchedwetsa chionongeko chawo

44Ndipo Ife tidatumiza Atumwi ena motsagana ndipo nthawi iliyonse Mtumwi amadza kwa iwo ndipo amamukana nati ndi wabodza. Ndipo Ife tidawaononga ena pambuyo pawo ndipo tidawapanga iwo kukhala chitsanzo cha mbiri ya anthu olakwa. Ichi chidali chionongeko cha anthu osakhulupirira

45Ndipo Ife tidamutumiza Mose pamodzi ndi m’bale wake Aroni ndi zizindikiro ndiponso ulamuliro wathu

46Kwa Farawo ndi nduna zake ndipo iwo adawalandira mwamwano chifukwa iwo adali anthu a chipongwe

47Ndipo iwo adati, “Kodi ife tikhulupirire anthu awiri olingana ndi ife amene anthu awo ndi akapolo athu?”

48Iwo adawakana iwo kotero iwo adalandira chionongeko

49Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku la Chipangano Chakale kuti anthu ake akhoza kutsogozedwa bwino

50Ife tidamupanga mwana wamwamuna wa Maria pamodzi ndi amayi ake kukhala chizindikiro kwa anthu onse ndipo tidawapatsa mnthunzi pa malo okwera ndi malo a mtendere amene anali kuthiriridwa ndi madzi a pa kasupe

51Oh Atumwi! Idyani zinthu zabwino ndipo muzichita ntchito zabwino. Ndithudi Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita

52Ndithudi chipembedzo chanu ndi chimodzi ndipo Ine ndine Ambuye wanu. Kotero ndiopeni Ine

53Koma anthu adagawanika m’magulu osiyanasiyana, gulu lililonse limasangalala ndi ziphunzitso zawo

54Alekeni ayambe achimwa mpaka pamene imfa iwapeza

55Kodi iwo amaganiza kuti popeza tawapatsa chuma ndi ana

56Ndiye kuti Ife tili kuwafunira zabwino? Iyayi. Iwo sadziwa kanthu ayi

57Ndithudi iwo ndi anthu amene amaopa Ambuye wawo

58Amene amakhulupirira zizindikiro za Ambuye wawo

59Amene sapembedza wina aliyense poonjezera pa Ambuye wawo

60Amene amapereka chaulere mitima ili yoopa Ambuye wawo chifukwa chakuti adzabwerera kwa Iye

61Awa ndiwo amene amapikisana wina ndi mnzake pochita zabwino ndipo amakhala oyamba pozindikira

62Ife sitinyamulitsa mzimu wina uliwonse katundu amene iwo sangathe kunyamula. M’buku lathu mudalembedwa zoona zokhazokha. Ndipo palibe munthu amene adzaponderezedwa

63Koma mitima ya anthu osakhulupirira siyizidziwa zimenezi ayi. Iwo ali ndi ntchito zina zoipa kupatula zimene iwo amachita

64Koma pamene chilango chathu chidza pa iwo amene amakhala mu mtendere, iwo adzafuula kufuna chithandizo

65Musalire tsiku la lero chifukwa inu simudzalandira chithandizo china chilichonse kuchokera kwa Ife

66Chivumbulutso changa chinali kulakatulidwa kwa inu nthawi zambiri koma inu munali kuthawa ndi kuchikana mwamwano

67Inu mumachinyoza usana ndi usiku uliwonse

68Kodi iwo sangathe kulingalira mozama pa mawu a Mulungu kapena pali china chake chimene chidavumbulutsidwa kwa iwo chimene sichidavumbulutsidwe kwa makolo awo

69Kapena iwo sadziwa kuti akukana Mtumwi wawo

70Kapena iwo akuti Iye ndi wopenga? Koma iye wawabweretsera iwo onse zoonadi. Koma ambiri amakana choonadi

71Kukadakhala kuti choonadi chimatsatira zofuna zawo, ndithudi, kumwamba, dziko lapansi ndi onse okhala m’menemo akadaonongeka. Ife tawapatsa chikumbutso komabe iwo safuna kumvera chikumbutsocho

72Kapena iwe uli kuwapemphera mphotho? Chithandizo cha Ambuye wawo ndicho chabwino. Ndipo Iye ndiye wopereka moolowa manja kuposa onse amene amapereka

73Ndithudi iwe uli kuwaitana kuti adze kunjira yoyenera

74Ndithudi iwo amene amakana moyo umene uli nkudza adzakhala ali kusochera ku njira yoyenerayi

75Ngati Ife tikadawalangiza chisoni chathu ndi kuwachotsera mavuto, iwo akadakhala ali kulakwabe m’njira zawo zoipa ndi kusokonezeka ndi zoipazo

76Ndithudi tidawalanga kale koma iwo sadafunefune Ambuye wawo kapena kukhala odzichepetsa pamaso pake

77Mpaka pamene tidzawatsekulira khomo la chilango chowawa, iwo adzakhala okhumudwa

78Iye ndiye amene adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Komabe inu simuthokoza mokwanira

79Iye ndiye amene adakulengani ndi kukuchulukitsani padziko lapansi ndipo nonsenu mudzasonkhanitsidwa kudza pamaso pake

80Iye ndiye amene amapereka moyo ndiponso imfa ndipo ndi Iyenso amene amasithanitsa usiku ndi usana. Kodi simungazindikire

81Iwo amanena zimene anthu akale ankanena

82Iwo amati, “Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, kodi tidzadzukanso ndi kukhala ndi moyo?”

83Ndithudi ife tidalonjedzedwa zimenezi kale pamodzi ndi makolo athu. Izi si zina ayi koma nkhani zabodza za anthu a makedzana

84Nena, “Kodi Mwini wake wa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo ndani? Ndiuzeni ngati mumudziwa.”

85Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Kodi inu simungachenjezedwe?”

86Nena, “Kodi Ambuye wa miyamba isanu ndi iwiri ndiponso Mwini Ufumu ndani?”

87Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Nanga kodi simungasiye kuchita zoipa?”

88Nena, “Kodi ulamuliro wa zinthu zonse zili m’manja mwa yani? Kodi ndani amene amaziteteza zonse pamene Iye safuna chitetezo cha wina aliyense ngati inu mukudziwa?”

89Iwo adzati, “M’manja mwa Mulungu.” Nena, “Nanga ndi chifukwa chiyani inu mwanyengedwa?”

90Iyayi, Ife tawavumbulutsira choonadi. Koma onsewa ndi anthu abodza

91Palibe nthawi imene Mulungu adabala mwana ndipo kulibe Mulungu wina woonjezera pa Iye. Ngati izi zikadakhala choncho, bwezi Mulungu aliyense akumatenga zolengedwa zake zokha ndi kumaziika pamwamba pa zolengedwa za Mulungu wina. Ulemerero ukhale kwa Mulungu woposa zina zilizonse

92Iye amadziwa zonse zooneka ndiponso zobisika. Mulungu akhale wopambana milungu ina imene iwo amaitumikira

93Nena, “Ambuye wanga! Ngati Inu mukadandionetsa chilango chimene muli kuwopseza

94Ambuye wanga! Pulumutsani ndipo musandisiye ine pakati pa mtundu wa anthu oipawu.”

95Ndithudi, Ife tili ndi mphamvu zoti ukhoza kuona chilango chimene tawaopseza

96Dzitetezeni ndi chabwino pothamangitsa choipa. Ife tili kudziwa zonse zimene ali kukunamizirani

97Ndipo iwe unene kuti, “Ambuye wanga, Ine ndili kufuna chitetezo chanu pothawa zoipa za Satana.”

98“Ambuye! Ine ndili kupempha chitetezo chanu kuti asabwere kumene ndili ine.”

99Mpaka pamene imfa idza kwa munthu wolakwa iye adzati, “Ambuye wanga! Bwezeni.”

100“Kuti ndikachite ntchitozabwinozimenendidalepherakuchita.” Kosatheka! Amenewa ndiwo mawu chabe amene akungolankhula. Kumbuyo kwawo kudzakhala chipupa mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa

101Ndipo pamene lipenga lidzaombedwa, pa tsiku limeneli, ubale wawo wonse udzathera pomwepo ndiponso sadzafunsana chithandizo chochokera kwa wina ndi mnzake

102Aliyense amene muyeso wake udzakhala wolemera, adzapambana

103Koma aliyense amene muyeso wake udzakhala wopepuka adzataya moyo wake ndipo adzakhala ku Gahena nthawi zonse

104Moto udzatentha nkhope zawo ndipo izo zidzakwinyikakwinyika chifukwa chaululu

105“Kodi chivumbulutso chathu sichidalakatulidwe kwa inu? Kodi simudachikane?”

106Iwo adzati, “Ambuye wathu! Zilakolako zathu zidatigonjetsa ife ndipo tidali anthu osochera.”

107“Ambuye wathu! tipulumutseni ife ku ichi. Ngati ife tidzabwereranso ku zoipa, ndithudi, ife tidzakhala anthu oipa kwambiri.”

108Iye adzati, “Khalani mu icho mwamanyazi ndipo musandiyankhulitse Ine ayi.”

109Ndithudi padali gulu la Atumiki anga amene adati, “Ambuye wathu! Ife timakhulupirira mwa inu. Tikhululukireni ndipo mutichitire chisoni. Inu ndinu wabwino pochita chisoni kuposa a chisoni onse.”

110Koma inu munali kuwanyogodola mpaka pamene inu mudandiiwala Ine ndipo inu munali kuwaseka iwo

111Ndithudi lero Ine ndawalipira chifukwa cha kupirira kwawo ndipo iwo ndi amene apambana

112Ndipo Iye adzafunsa kuti, “Kodi inu munakhala padziko lapansi zaka zingati?”

113Iwo adzayankha kuti, “Takhala tsiku limodzi kapena mphindi zochepa zokha. Afunseni iwo amene amasunga chiwerengero.”

114Iye adzawayankha kuti, “Inu mukadadziwa ndi nthawi yochepa kwambiri imene inu munakhala.”

115“Kodi inu mumaganiza kuti tidangokulengani inu opanda cholinga ndipo kuti simudzabwerera kwa Ife?”

116Motero alemekezeke Mulungu, Mfumu ya chilungamo. Palibe Mulungu wina koma Iye yekha, Ambuye wa Mpando wolemekezeka ndi Wachifumu

117Aliyense amene apembedza mulungu wina woonjezera pa Mulungu, pamene Iye alibe umboni wa chimenecho, Ambuye wake adzamufunsa. Ndithudi anthu osakhulupirira sadzapambana ayi

118Nena, “Ambuye wanga! Ndikhululukireni machimo anga ndipo mundichitire chisoni chifukwa Inu ndinu wachisoni choposa a chisoni onse.”

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath