18. Al-Kahf
1Kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu amene wavumbulutsa kwa kapolo wake Buku ndipo sanaike mu ilo zokayikitsa zina zili zonse
2Lolungama kuti lichenjeze za chilango chowawa chochokera kwa Iye ndi kuwauza anthu okhulupirira amene amachita ntchito zabwino kuti adzalandira mphotho yabwino
3M’menemo adzakhalamo mpaka kalekale
4Ndi kuchenjeza iwo amene amanena kuti, “Mulungu wabereka mwana wamwamuna.”
5Pa izi iwo sadziwa china chilichonse, ngakhale makolo awo. Loopsa ndi liwu lalikulu limene likutuluka m’kamwa mwawo. Iwo sanena china koma bodza
6Mwina iwe ukhoza kudzipha ndi chisoni chifukwa chakuti iwo sakhulupirira chivumbulutsochi
7Ndithudi! Ife tazipanga zimene zili m’dziko lapansi kukhala zokongola ndi cholinga chakuti tiwayese kuti ndani mwa iwo ali wochita zabwino
8Ndithudi! Ife tidzapanga zonse zimene zili pa dziko kukhala nthaka youma
9Kodi iwe ukuganiza kuti anthu a ku phanga ndi malembo a pa gome ndi zozizwitsa pakati pa zizindikiro zathu
10Pamene anyamata adathawa ndipo adalowa ndi cholinga chopeza malo kuphanga ndipo adati, “Ambuye wathu! Tionetseni chisoni chochokera kwa Inu ndipo tikonzereni zinthu zathu munjira zoyenera.”
11Motero Ife tidawatseka makutu awo pamene anali kuphanga zaka zingapo
12Ndipo Ife tidawadzutsa kuti tidziwe ndani mwa magulu awiriwa amene adasunga bwino nthawi imene iwo adakhala kuphanga
13Ife tili kukuuza nkhani zawo zonse mwachoonadi. Ndithudi! Iwo anali anyamata amene adakhulupirira mwa Ambuye wawo, ndipo Ife tidawaonjezera malangizo
14Ndipo Ife tidalimbitsa mitima yawo, pamene adaima ndi kunena kuti, “Ambuye wathu ndiye Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi. Ife sitidzapembedza mulungu wina kupatula Iye yekha. Ngati tikatero ndiye kuti tayankhula bodza lopyola muyeso.”
15Awa anthu athu amatumikira milungu ina yoonjezera pa Iye. Kodi ndi chifukwa chiyani iwo sawabweretsera umboni woonekera weniweni? Kodi wochimwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu
16Pamene inu muwapewa iwo pamodzi ndi zimene iwo akupembedza osati Mulungu, thawirani kuphanga kuti mukapeze mpumulo. Ambuye wanu adzakutambasulirani chisoni chake ndi kukukonzerani njira yoti zinthu zikupepukireni
17Mwina iwe udaona dzuwa pamene linali kutuluka kupita ku mbali ya manja kwa phanga lawo ndipo pamene linali kulowa lilikudutsa ku mbali ya manzere, iwo adagona m’kati mwake. Chimenecho ndi chimodzi cha zizindikiro za Mulungu. Yense amene Mulungu amutsogolera ndi wotsogozedwa bwino koma iye amene Iye amusocheza, iwe siungam’pezere bwenzi woti amutsogolere
18Ndipo inu mukadaganiza kuti iwo adali maso pamene iwo adali mtulo. Ndipo Ife tinali kuwatembenuza kuchoka ku mbali ya manja kupita ku mbali ya manzere ndipo galu wawo adali chigonere ndi miyendo yake iwiri ya m’tsogolo ili yotambasula pa khomo la phanga. Iwe ukadaona iwo ukadachita mantha ndipo ukadathawa. Ndithudi iwe ukadadzadzidwa ndi mantha chifukwa cha iwo
19Chomwecho Ife tidawadzutsa kuti afunsane wina ndi mnzake. Wina wa iwo adafunsa nati, “Kodi inu mwakhala nthawi yotani? Iwo adayankha kuti: ‘Ife takhala tsiku limodzi kapena theka la tsiku.’ Iwo adati: “Ambuye wanu ndiye amene adziwa bwino za nthawi imene mwakhala kuno. Mtumizeni mmodzi wa inu ku mzinda ndi ndalama zanu za siliva kuti akagule chakudya chabwino kuti akubweretsereni. Koma akasamale ndipo asakauze aliyense za inu.”
20“Chifukwa ngati iwo adzadziwa za inu, adzakuponyani miyala kapena adzakubwezerani ku chipembedzo chawo. Ndipo zitatero inu simudzapambana ayi.”
21Motero Ifetidawadziwitsaanthuzaiwokutiiwoakhoza kudziwa kuti pangano la Mulungu ndi loona, ndipo kuti ola la chionongeko, ndithudi, lidzadza popanda chikayiko. Nthawi imene amakangana pa nkhani zawo za kuphanga iwo adati; ‘Amangireni nyumba pakhomo la phanga lawo. Ambuye wawo yekha ndiye amene adziwa za iwo.’ Ndipo iwo amene adapambana pa zochita zawo anati: “Ndithudi Ife tidzamanga malo opembedzerapo pamalopo.”
22Ena a iwo adati, Adali atatu ndipo galu wawo adali wachinayi, pamene ena akuti adali asanu ndipo galu wawo adali wachisanu ndi chimodzi. Moganizira zinthu zobisika, ena akuti adalipo asanu ndi awiri ndipo galu wawo adali wachisanu ndi chitatu. Nena, “Ambuye wanga ndi wodziwa kwambiri chiwerengero chawo, palibe amene akuwadziwa kupatula ochepa okha.” Usakangane nawo za iwo kupatula mkangano womveka. Ndipo usamufunse wina aliyense wa anthu zokhudza anthu a kuphanga
23Ndipo usanene za china chilichonse kuti, “Ine ndidzachita ichi mawa.”
24Opanda kuonjezera mawu oti, “Ngati Mulungu afuna.” Ndipo kumbukira Ambuye wako ngati uiwala ndipo unene kuti, “Ngati ndikotheka Mulungu anditsogolere ine ndi kundibweretsa kufupi ndi choonadi m’malo mwa ichi.”
25Iwo adakhala m’phanga lawo zaka mazana atatu ndi kuonjeza mphambu zisanu ndi zinayi
26Nena, “Mulungu amadziwa kwambiri mmene adakhalira. Kudziwa zinsinsi zonse za kumwamba ndi za dziko lapansi ndi kwake. Oh! Iye amapenyetsetsa ndipo amamvetsetsa. Iwo alibe wina woti awasamale oposa Mulungu. Ndipo Iye samuphatikiza wina aliyense mu ulamuliro wake.”
27Werenga zimene zavumbulitsidwa kwa iwe m’Buku la Ambuye wako. Palibe munthu amene angasinthe mawu ake. Iwe siudzapeza kothawira kupatula kwa Iye
28Pirira pamodzi ndi iwo amene akupembedza Ambuye wawo m’mawa ndi madzulo kufuna chisangalalo chake. Maso ako asayang’ane kutali kuwasiya iwo ndi cholinga chakuti upeze zinthu zabwino m’moyo uno ndipo usamumvere iye amene mtima wake tauiwalitsa kuti asamatikumbukire; ndipo watsatira zofuna za mtima wake, ndipo ntchito zake zonse ndi zoonongeka
29Nena, “Choonadi chimachokera kwa Ambuye wanu. Amene afuna akhulupirire ndipo amene safuna akane. Ndithudi anthu oipa tawakonzera moto umene mphanda zake zidzawazungulira.” Pamene iwo adzapempha madzi akumwa adzapatsidwa madzi otentha ngati mkuwa wosungunuka amene adzaotcha nkhope zawo. Kuipa kwa chakumwa ndi kuipa kwa malo okhala ndi kumeneku
30Kwa iwo amene akhulupirira nachita zabwino, ndithudi, Ife sitidzaononga mphotho ya anthu ochita zabwino
31Iwo adzakhala m’minda yamuyaya ndipo mitsinje izidzayenda pansi pawo. Iwo adzavekedwa zibangiri za golide ndipo adzavala nsalu za sirika wobiriwira, wopepuka ndi wochindikala ndipo adzatsamira pa masofa ndipo malipiro abwino ndi malo abwino ofikira
32Auze za fanizo la anthu awiri. Mmodzi wa iwo adali ndi minda iwiri ya mphesa imene tidazunguliza m’mbali mwake ndi mitengo ya tende ndipo tidaika pakati pake mbewu zina
33Munda uliwonse umapereka zipatso zake, ndipo siupunguza chilichonse ndipo Ife tidatumphutsa mitsinje m’kati mwa mindayo
34Ndipo Iye adali ndi zipatso zambiri ndipo adanena kwa mnzake pamene anali kutsutsana naye nati, “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe ndiponso ndili ndi anthu a ntchito amphamvu kwambiri.”
35Ndipo iye adalowa m’munda mwake modzitukumula yekha nati, “Ine sindiganiza kuti izi zidzatha ayi.”
36“Ndipo ine sindikhulupirira kuti ola la chionongeko lidzadza. Ndipo ngakhale nditabwezedwa kwa Ambuye wanga, ine ndikapeza malo abwino oposa awa.”
37Mnzake uja adati kwa iye, “Kodi iwe wam’kana Iye amene adakulenga iwe kuchokera ku dothi ndi kuchokera ku dontho la umuna ndipo adakuumba kukhala munthu?”
38Akakhala ine, Mulungu ndiye Ambuye wanga. Ine sindidzamufanizira Iye ndi china chilichonse
39Bwanji pamene iwe umalowa m’munda mwako, siudanene kuti, “Izi ndi zimene Mulungu wafuna ndipo kulibe mphamvu kwina kulikonse kupatula kwa Mulungu? Ngakhale iwe ukundiona ine kuti ndine wochepekedwa kwambiri m’chuma ndi ana.”
40“Mwina Ambuye wanga akhoza kundipatsa munda wabwino oposa wako ndi kutumiza ziphaliwali kuchokera kumwamba ndi kusandutsa nthaka kukhala yosabereka.”
41“Kapena kuzamitsa madzi ake kuti iwe usawapeze.”
42Ndipo zipatso zake zidaonongeka. Ndipo iye adayamba kufikisa zikhato zake mwachisoni chifukwa cha zonse zimene adaononga pa mindayi chifukwa zonse zidaonongeka. Ndipo iye adati: “Kalanga ine! Ndikanadziwa, sindikanaphatikiza milungu ina ndi Ambuye wanga!”
43Ndipo iye adalibe gulu lomuthandiza polimbana ndi Mulungu ndiponso adalibe mphamvu zoti adzitetezere kapena kudzipulumutsira
44Kumeneko chitetezo chidzakhala chochokera kwa Mulungu, Mwini choonadi. Iye ndiye ali ndi malipiro ndiponso mapeto abwino
45Uwapatse chitsanzo cha moyo wa padziko lapansi. Moyowu uli ngati madzi amene timatsitsa kumwamba ndi mbeu za padziko la pansi zimene zimasakanizana ndi iwo ndipo zimakhala zanthete ndi zobiliwira. Koma pambuyo pake zimauma ndi kufumbutuka ndipo mphepo imazimwaza. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse
46Chuma ndi ana ndi zinthu zokongola za umoyo wadziko lapansi. Koma ntchito zabwino zokhalitsa ndi zomwe zili ndi malipiro abwino kwa Ambuye wako ndi chiyembekezo chabwino
47Ndi tsiku limene tidzagudubuza mapiri ndipo mudzaona nthaka ili kukhala poyera popanda chilichonse ndipo Ife tidzasonkhanitsa anthu onse. Palibe aliyense amene tidzamusiye mwa iwo
48Ndipo iwo adzaonetsedwa kwa Ambuye wako ataimikidwa m’mizere ndipo tidzanena kuti, “Ndithudi inu mwabwera kwa Ife monga momwe tidakulengerani poyamba. Koma inu munali kuganiza kuti lonjezo lathu silidzakwaniritsidwa ayi.”
49Ndipo Buku lidzaikidwa m’manja mwa aliyense ndipo iwe udzaona anthu ochita zoipa ali ndi mantha poona zonse zimene zidalembedwa mu Bukulo. Iwo adzati, “Tsoka kwa ife! Kodi Buku ili ndi lotani limene silisiya kanthu kakang’ono kapena kakakulu ndipo zonse lidasunga?” Ndipo iwo adzapeza ntchito zawo zonse zitalembedwa momwemo ndipo Ambuye wako sadzapondereza wina aliyense
50Pamene Ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Motero onse anamugwadira Iye kupatula Satana amene adali mmodzi wa ziwanda ndipo adanyoza lamulo la Ambuye wake. Kodi mudzasankha iyeyo pamodzi ndi ana ake kukhala okutetezani ndi kukuthandizani m’malo mwa Ine, pamene iwo ndi adani? Kodi ndi choipa chotani chimene anthu ochita zoipa asankha
51Ine sindidawaonetse kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi kapena kalengedwe kawo komwe ndiponso Ine sindidawasankhe, osocheretsa anthu, kukhala ondithandiza anga
52Ndi tsiku limene Iye adzati kwa iwo, “Itanani onse amene mumandifanizira aja, amene munkadzinamiza aja.” Ndipo iwo adzalira kwa iwo koma sadzawayankha ndipo Ife tidzabzala chidani pakati pawo
53Ndipo anthu ochimwa adzaona moto wa ku Gahena ndipo adzatsimikiza kuti iwo aulowa. Ndipo iwo sadzapeza njira yothawirako
54Ndithudi Ife tawakhazikitsira anthu chitsanzo chilichonse mu Korani ino. Koma munthu ndi wotsutsa muzinthu zambiri
55Palibe chimene chimawaletsa anthu kukhulupirira ndi kupempha chikhululukiro kwa Ambuye wawo pamene chilangizo chidza kwa iwo kupatula kuti ali kudikira njira za anthu a zaka zakale kuti ziwapeze iwo kapena kuti akumane ndi mazunzo maso ndi maso
56Ndipo Ife sitimangotumiza Atumwi kupatula kuti akalalikire nkhani yabwino ndi kupereka chenjezo. Koma anthu osakhulupirira amatsutsa mwabodza kuti agonjetse choonadi ndi bodza lawo. Ndipo iwo amasandutsa mawu anga ndi zonse zomwe achenjezedwa ngati nthabwala kapenachoseketsa
57Kodiwolakwakwambirindanikuposa munthu amene akakumbutsidwa mavesi a Ambuye wake iye amawakana ndi kuiwala zimene manja ake atsogoza? Ife taika zophimba mitima yawo kuti asazindikire ndipo tatseka m’makutu mwawo. Ndipo ngati iwe utawaitana iwo kuti atsatire njira yoyenera, iwo sadzatsogozedwa
58Ndipo Ambuye wako ndi wokhululukira kwambiri ndi Mwini chisoni. Iye akadafuna kuwalanga chifukwa cha machimo amene achita, ndithudi, Iye akadawafulumizitsira chilango chawo. Koma iwo ali ndi nthawi yawo ndipo sadzapeza kothawirako
59Ndi Mizinda, imene tidaiononga pamene eni ake adachita zoipa tidaika nthawi yachionongeko chawo
60Ndipo pamenepo Mose adamuuza mnyamata wake kuti, “Ine ndidzapitirirabe kuyenda mpaka pamene ndidzafika pamalo pamene nyanja ziwiri zikumana kapena ndidzapitirira kuyenda zaka ndi zaka.”
61Koma pamene iwo adafika pamalo pamene nyanja ziwiri zidakumana, iwo adaiwala nsomba yawo ndipo iyo idatenga njira yake yodutsa kupita m’madzi
62Ndipo iwo atapitiriza ulendo wawo, Mose adati kwa mnyamata wake, “Bweretsa chakudya chathu. Ndithudi tapeza, mu ulendo wathu, zotopetsa.”
63Iye adati, “Kodi iwe siudaone pathanthwe pamene tidapuma paja, kuti ine ndidaiwala nsomba ndipo palibe china chimene chidandiiwalitsa kuti ndiikumbukire koma Satana yemwe adandiiwalitsa. Ndipo iyo idalowa m’madzi mozizwitsa.”
64Mose adati, “Pamenepo ndi pamene timafuna.” Iwo adabwerera kulondola kumene adachokera
65Ndipo iwo adam’peza mmodzi wa akapolo wathu amene tidamupatsa chifundo chochokera kwa Ife ndiponso tidamuphunzitsa nzeru zochokera kwa Ife
66Mose adati kwa iye, “Kodi ndingakutsateni kuti mwina mundiphunzitse zabwino zina za zimene mudaphunzitsidwa?”
67Iye adati, “Ndithudi! Iwe siudzatha kupirira ndi ine.”
68Kodi iwe ungapirire bwanji pa zinthu zimene suli kuzidziwa
69Mose adati, “Ngati Mulungu afuna, udzandipeza ine ndili wopirira ndipo ine sindidzakunyoza iwe ayi.”
70Iye adati, “Ngati iwe unganditsatire, usandifunse china chilichonse chimene ungawone mpaka pamene ine nditakuuza za chinthucho.”
71Motero iwo adanyamuka ndipo pamene iwo adakwera m’chombo, mnzake wa Mose adaboola chombocho. Mose adati, “Kodi waboola dzenje pa chombochi ndi cholinga chofuna kumiza eni ake? Ndithudi ichi ndi chinthu choipa kwambiri chimene wachita!”
72Iye adati, “Kodi sindidakuuze kuti iwe siudzatha kupirira ndi ine?”
73Mose adati, “Musandidzudzule chifukwa cha zimene ndaiwala ndipo musandisenzetse katundu wolemera chifukwa cha zochita zanga.”
74Ndipo onse adapitirizabe ulendo wawo mpaka pamene adakumana ndi mnyamata wina amene iye adamupha. Ndipo Mose adati, “Kodi iwe wapha munthu wosalakwa amene sadaphepo wina aliyense? Ndithudi iwe wachita chinthu choipa kwambiri.”
75Iye adati, “Kodi ine sindidakuuze kuti iwe siudzatha kupirira ndi ine?”
76Mose adati, “Ngati ine ndikufunsanso chinthu china pambuyo pa izi, usayende nanenso chifukwa ukhala utachipeza chifukwa kuchokera mwa ine.”
77Ndipo onse adapitirira kuyenda mpaka pamene adapeza anthu a mu mzinda wina wake ndipo iwo adawafunsa anthu aja kuti awapatseko chakudya koma iwo adakana kuwalandira ngati alendo awo. Iwo adapeza mu mzindawo chipupa chikufuna kugwa ndipo Iye adachimanganso. Mose adati, “Iwe ukadafuna, ndithudi, ukadawauza kuti akulipire chifukwa cha ntchito imene wagwira.”
78Iye adati, “Uku ndiye kusiyana kwa pakati pa iwe ndi ine. Ndikuuza tanthauzo la zinthu zimene iwe umakanika kupirira nazo.”
79Chikakhala chombo chija eni ake adali anthu osauka amene amagwira ntchito pa nyanja. Ndipo ine ndinafuna kuti ndichiononge chifukwa kutsogolo kwawo kudali mfumu yomwe imalanda chombo chilichonse mwamphamvu
80Akakhala mnyamata uja, makolo ake onse adali okhulupirira mu choonadi ndipo timaopa kuti mwina iye akhoza kuwatembenuza ndi kuyamba kuchita zoipa ndi kusiya kukhulupirira
81Ndipo tidafuna kuti Ambuye wawo awapatse m’malo mwake, mwana wina wabwino ndi woyera mtima kuposa iye
82Chikakhala chipupa chija, eni ake adali ana awiri a masiye amene amakhala mu mzinda uja ndipo pansi pa chipupacho padali chuma chawo. Ndipo bambo wawo adali munthu wabwino motero Ambuye wako adafuna kuti anawo akule kuti adzatulutse okha chuma chawo ngati chifundo chochokera kwa Ambuye wako. Ine sindidachite zimenezi mwachifuniro changa ayi. Limeneli ndilo tanthauzo lake la zinthu zimene umalephera kupirira nazo
83Ndipo iwo akukufunsa za Dhul-Qarnain. Nena, “Ine ndikufotokozerani za mbiri ya iye.”
84Ndithudi Ife tidamukhazika iye padziko ndipo tidamupatsa njira yopezera chilichonse
85Ndipo iye adatsatira njira
86Mpaka pamene adafika polowera dzuwa ndipo adalipeza dzuwalo lili kulowa m’dziwe la matope akuda. Pafupi pomwepo iye adapeza anthu ena. Ife tidati, “Iwe Dhul-Qarnain! Iwe uli ndi ufulu wowalanga kapena wowachitira chisoni.”
87Iye adati, “Akakhala iye amene achita zoipa, tidzamulanga ndipo iye adzabwezedwa kwa Ambuye wake yemwe adzamulanga ndi chilango choipa kwambiri.”
88Koma iye amene wakhulupirira ndikumachita ntchito zabwino, adzakhala ndi mphotho yabwino ndipo tidzamuyankhula mawu abwino
89Ndipo iye adatsatira njira ina
90Mpaka pamene adafika kotulukira dzuwa kumene adalipeza dzuwa lili kutuluka pa anthu amene Ife sitidawaikire chotchinga ku dzuwa
91Kotero Ife tidadziwa zonse zokhudza iye
92Ndipo iye adatsatiranso njira ina
93Mpaka pamene iye adafika pakati pa mapiri awiri adapeza pambali pake anthu amene sanali kuzindikira chilichonse
94Iwo adati, “Iwe Dhul-Qarnain! Ndithudi Ya-juj ndi Majuj ali kuchita zoipa m’dziko lino. Kodi tikupatse malipiro kuti utimangire linga lotiteteza nalo pakati pa iwo ndi ife?”
95Iye adati, “Mphamvu zomangira linga zimene Ambuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi anthu amphamvu ogwira ntchito kuti ndimange linga pakati pa inu ndi iwo.”
96Ndipatseni zidutswa zachitsulo; mpaka pamene iye adadzadza gawo limene linali pakati pa mapiriwa. Iye adati, “Uzirani ndi livumbo lanu.” Pamene adazifiwiritsa zidutswazo ngati moto, iye adati, “Ndipatseni mtovu kuti ndiuthire pa zidutswazo.”
97Anthu a Ya-juj ndi Majuj sadathe kuchilumpha ndipo sadathe kuchiboola
98Iye adati, “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Ambuye wanga. Koma pamene lonjezo la Ambuye wanga lidzadza, Iye adzaliononga. Ndipo lonjezo la Ambuye wanga ndi loona
99Ndipo pa tsikulo tidzawasiya ena mwa iwo akusakanikirana ndi ena. Lipenga lidzaimbidwa ndipo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi
100Pa tsiku limeneli tidzaonetsa Gahena kwa anthu osakhulupirira, kuti adzalione lonse moonekera kwambiri
101Amene maso awo adali otsekeka kuchikumbutso changa, satha kumva
102Kodi anthu osakhulupirira akuganiza kuti akhoza kuwapanga akapolo anga kukhala atetezi awo m’malo mwa Ine? Ndithudi Ife takonza Gahena kukhala malo ofikira anthu onse osakhulupirira
103Nena, “Kodi tikuuzeni anthu amene ali olephera mu ntchito zawo?”
104Iwowo ndi amene ntchito zawo zaonongeka m’moyo uno pamene iwo anali kuganiza kuti ali kulandira zabwino chifukwa cha ntchito zawo
105Iwo ndi amene sadakhulupirire mawu a Ambuye wawo ndi zokumana ndi Iye. Motero ntchito zawo zaonongeka ndipo patsiku lachiweruzo Ife sitidzawakhazikira muyeso
106Gahena idzakhala mphotho yawo chifukwa iwo adalibe chikhulupiriro ndipo achitira chipongwe Atumwi ndiponso mawu anga
107Ndithudi! Iwo amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, minda ya ku Paradiso idzakhala malo awo ofikira
108Adzakhala komweko nthawi zonse ndipo sadzafuna kusintha malo
109Nena, “Ngati Nyanja ikadakhala inki yolembera mawu Ambuye wanga, ndithudi, nyanjayo ikadaphwa koma osati Mawu a Ambuye wanga ngakhale tikadabweretsa nyanja yofanana ndi imeneyo moonjezera.”
110Nena, “Ine ndine munthu monga inu nomwe, koma zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi. Kotero aliyense amene afuna kudzakumana ndi Ambuye wake ayenera kuchita zimene zili zabwino ndipo popembedza Ambuye wake, osaphatikizamo wina wake.”
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath