Chisilamu
kubwerera

17. Al-Israa

1Ulemerero ukhale kwa Iye amene adayendetsa kapolo wake nthawi ya usiku kuchoka ku Mzikiti Wolemekezeka kupita ku Mzikiti wakutali umene malo ake ozungulira tidawadalitsa; kuti timuonetse zina za zizindikiro zathu. Ndithudi Iye ndiwakumva ndipo woona zonse

2Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku ndipo tidalipanga ilo kukhala chilangizo cha ana a Israyeli ponena kuti, “Musasankhe wina aliyense kupatula Ine kukhala wokutetezani.”

3oh inu ana a iwo amene tidawanyamula pamodzi ndi Nowa! Ndithudi Iye adali kapolo wothokoza kwambiri

4Ife tidavumbulutsa kwa ana a Israyeli, m’Buku kuti, mosakayika, inu mudzabweretsa chisokonezo padziko kachiwiri ndipo mudzakhala ankhanza ndi odzikweza kwambiri

5Ndipo litadza pangano loyamba, Ife tidzakutumizirani akapolo athu a gulu la nkhondo ankhongono zedi. Iwo amalowa m’katikati mwa nyumba zanu. Ndipo linali lonjezo limene linakwaniritsidwa

6Titatero tidakupatsani mphamvu powagonjetsa iwo. Ndipo tidakuonjezerani chuma ndi ana ndipo tidakupangani kukhala anthu ambiri amphamvu

7Ngati inu muchita zabwino, mukudzichitira nokha ubwinowo, koma ngati muchita zoipa, mukudzichitiranso nokha. Ndipo pamene pangano lomaliza lidza, Ife tidzalola adani anu kuti akumvetseni chisoni ndi kulowa mu Mzikiti wanu monga momwe adaloweramo koyamba ndi kukantha kwenikweni onse amene adawapeza

8Mwina Ambuye wanu adzakuchitirani chifundo koma ngati inu mubwerera kuuchimo, nafenso tidzabwezera kukanthani. Ife takonza Gahena kukhala ndende ya anthu osakhulupirira

9Ndithudi Korani ino imatsogolera ku zinthu zabwino ndipo imawauza anthu okhulupirira, amene amachita zabwino, kuti adzakhala ndi malipiro aakulu

10Ndipo iwo amene sakhulupirira za tsiku lotsiriza Ife tawakonzera chilango chowawa

11Ndipo munthu amapempha zoipa monga momwe amapemphera zabwino ndipo munthu ndi wopupuluma

12Ndipo tidapanga usiku ndi usana kukhala zizindikiro zathu ziwiri. Ndipo tidakuta chizindikiro chausiku ndi mdima pamene tidaika chizindikiro chamasana kukhala chooneka kuti inu muzifunafuna zabwino zochokera kwa Ambuye wanu, komanso kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero. Ndipo zinthu zonse tazifotokoza momveka

13Ndipo Ife tidamangirira ntchito za munthu aliyense pakhosi lake ndipo patsiku lachiweruzo tidzamutulutsira buku limene adzalipeze lili lotsekulidwa

14werenga Buku lako. Lero pakwana kuti mzimu wako udziwerengere wokha zonse zimene unkachita

15Aliyense amene achita zabwino atero podzipulumutsa yekha. Ndipo aliyense amene achita zoipa, atero podzipweteka yekha. Palibe amene adzanyamula katundu wa mnzake. Ndipo Ife sitilanga pokhapokha ngati tatumiza Mtumwi

16Ndipo pamene Ife tifuna kuononga Mzinda, poyamba timatumiza ulamuliro wathu kwa anthu ake opeza bwino. Ndipo iwo amauphwanya, ndipo motero liwu la chilango limatsimikiza pa iwo. Ndipo Ife timauononga kwambiri

17Kodi ndi mibadwo ingati ya anthu imene taononga pambuyo pa Nowa? Ambuye wako wakwana kukhala Wozindikira ndi woona zolakwa za akapolo ake

18Aliyense amene afuna chisangalalo cha msanga Ife timapereka msanga chimene Ife tifuna kwa amene Ife tamufuna. Ndipo pambuyo pake tamukonzera iye Gahena, imene adzalowa monyozedwa ndi mokankhidwa

19Ndipo yense amene afuna moyo umene uli nkudza, ndi kumaugwirira ntchito zake molimbika, ndipo ndi wokhulupirira, amenewo ndi amene ntchito zawo zidzakhala zoyamikidwa

20Ife timapereka kuchokera ku mphatso za Ambuye wako. Ndipo mphatso za Ambuye wako sizokanizidwa kwa aliyense

21Taona mmene tawalemekezera ena kuposa anzawo ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza uli ndi ulemu wambiri ndipo ndi waukulu poyerekeza

22Musasankhe mulungu wina ndi kumuphatikiza ndi Mulungu weniweni chifukwa mungadzakhale ndi manyazi ndi wopanda wokuthandizani

23Ndipo Ambuye wako walamula kuti musapembedze wina aliyense koma Iye yekha. Ndipo kuti muwachitire makolo anu zabwino. Ngati wina wa iwo kapena onse akalamba ali kukhala nanu, musawakalipire ayi, koma muziwayankhula ndi mawu aulemu

24Onetsani kudzichepetsa ndi chisoni ndipo munene kuti, “Ambuye wanga! Achitireni chifundo monga momwe iwo adandilerera pamene ine ndidali wamng’ono.”

25Ambuye wanu amadziwa kwambiri zonse zimene zili m’mitima mwanu. Ngati muli abwino ndithudi Iye ali wokhululukira kwa anthu amene amadza kwa Iye nthawi zonse modzichepetsa ndi kulapa

26Ndipo apatseni abale anu ndi anthu ovutika gawo lawo lowayenera ndiponso a paulendo amene avutika. Ndipo musapereke chuma chanu moononga

27Ndithudi anthu oononga ndi abale a Satana ndipo Satana, kwa Ambuye wake, ndi wosayamika

28Ndipo ngati iwe siuwathandiza ndipo uli kuyembekezera chisomo chochokera kwa Ambuye wako, yankhula nawo mwachifundo ndi mawu oleza

29Ndipo musakhale oumira kapena opereka moononga chifukwa mungadzudzulidwe kapena kukhala osauka kwambiri

30Ndithudi Ambuye wako amapereka zambiri kwa aliyense amene wamufuna ndipo amanyalapsa. Ndithudi Iye, kwa akapolo ake, ndi wodziwa ndi woona

31Ndipo musawaphe ana anu chifukwa choopa umphawi. Ife timawapatsa zosowa zawo ndi inu nomwe. Ndithudi kuwapha iwo ndi tchimo lalikulu

32Ndipo musayandikire chigololo. Ndithudi icho ndi chonyansa ndiponso njira yoipa

33Ndipo musaphe wina aliyense amene Mulungu waletsa pokhapokha ngati pali chifukwa chololedwa. Ndipo aliyense amene waphedwa mopanda chilungamo, Ife tamupatsa m’bale wake mphamvu zobwezera kapena kukhululuka pa imfa yake. Koma m’bale wakeyo asapyole muyeso pa kubwezeraku. Ndithudi iye ndi wotetezedwa

34Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye kupatula ngati muli ndi cholinga chochisamala mpaka pamene mwini wake adzafike pa msinkhu woti akhoza kuchisamalira yekha. Ndipo kwaniritsani lonjezo lililonse. Ndithudi! mudzafunsidwa za lonjezoli

35Ndipo kwaniritsani muyeso pamene muyesa zinthu ndipo yesani mwachilungamo polinga zinthu pa sikelo. Zimenezo ndizo zabwino ndipo ndi mapeto abwino kwambiri

36Ndipo musatsatire zinthu zimene simuzidziwa. Ndithudi kumvera kapena kuyang’ana kapenanso kuganizira kwa mumtima mwa munthu kudzafufuzidwa pa tsiku lachiweruzo

37Ndipo musayende modzitukumula pa dziko lapansi, ndithudi, inu simungathe kuboola nthaka ndi kufika kutalika kwa mapiri

38Kuipa kwa zonsezi sikukondweretsa Ambuye wako

39Ili ndi gawo la luntha limene Ambuye wako wakuuza iwe. Ndipo usatumikire mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa mwina iwe ungaponyedwe ku Gahena, modzudzulidwa ndi mokankhidwa

40Kodi Ambuye wanu wakusankhirani inu ana aamuna ndipo wadzisankhira Iye mwini ana aakazi kuchokera kwa Angelo? Ndithudi! Inu mukuyankhula mawu oopsa

41Ndithudi Ife tafotokoza chinthu chilichonse m’Korani iyi kuti iwo achenjezedwe, koma iyo siili kuonjezera chilichonse koma kuipidwa

42Nena, “Kukadakhala kuti kuli milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, monga momwe akunenera, iyo ikadapeza njira yoti ikhale pafupi ndi Mulungu.”

43Kuyamikidwa ndi kukhala pamwamba, kukhale kwake! Kuchokera ku bodza lalikulu limene iwo ali nkunena

44Miyamba isanu ndi iwiri, dziko lapansi ndi zonse zimene zimakhala m’menemo zimamulemekeza Iye ndipo palibe chinthu chomwe sichimulemekeza Mulungu. Koma inu simumva mayamiko. Ndithudi Iye ndi woleza mtima ndipo ndi wokhululukira nthawi zonse

45Pamene iwe umawerenga Korani, Ife timaika, pakati pa iwe ndi iwo amene sakhulupirira za moyo umene uli nkudza tchingo losaoneka

46Ndipo Ife taika zophimba m’mitima mwawo kuti mwina angaizindikire ndi m’makutu mwawo kuti asaimvetse. Ndipo pamene iwe utchula Ambuye wako yekha mu Korani iwo amatembenuka kuthawa mosangalala

47Ife timadziwa kwambiri zimene iwo akumva ndi pamene amamvetsera kwa iwe. Ndipo pamene amanong’onezana, taona anthu oipa, amanena kuti: “Inu mukutsatira munthu wolodzedwa.”

48Taona mmene akuperekera zitsanzo zokhudza iwe. Motero iwo asochera ndipo sangathe kupeza njira

49Ndipo iwo amati, “Kodi pamene ife tidzasanduka mafupa ndi zidutswa zopereseka kodi tidzaukitsidwanso kukhala chilengedwe chatsopano?”

50Nena, “Khalani miyala kapena zitsulo.”

51“Kapena cholengedwa china chimene ndi chachikulu m’mitima mwanu.” Iwo adzati, “Ndani amene adzatibwezeranso?” Nena, “Iye amene adakulengani poyamba.” Ndipo iwo adzapukusa mitu yawo ndipo kwa iwe adzafunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitika liti?” Nena, “Mwina zili pafupi.”

52Pa tsiku limene Iye adzakuitanani ndipo inu mudzamuyankha ndi matamando ake ndi kumvera, pamenepo inu mudzaganiza kuti simudakhale nthawi yaitali koma yochepa

53Auze akapolo anga kuti aziyankhula zokhazo zimene zili zabwino. Ndithudi Satana amafesa chidani pakati pawo. Ndithudi Satana, kwa munthu, ndi mdani woonekeratu

54Ambuye wanu amadziwa kwambiri za inu ndipo ngati Iye afuna adzakuchitirani chifundo kapena ngati Iye afuna adzakulangani. Ndipo Ife sitidakutumize iwe kuti ukhale wowayang’anira iwo ayi

55Ambuye wako amadziwa kwambiri zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi ndipo, ndithudi, Ife tidalemekeza Aneneri ena kuposa anzawo ndipo kwa Davide, Ife tidamupatsa Buku la Masalimo

56Nena, “Aitaneni onse amene mumadzinyengeza nawo mowonjezera pa Iye. Iwo alibe mphamvu zochotsa mavuto anu kapena kuwasintha ndi kupatsa munthu wina.”

57Iwo amene amawapembedza nawonso amafunafuna njira yodziyandikiritsira kwa Ambuye wawo, kuti ndani amene angakhale pafupi kwambiri ndi Mulungu ndipo amafunafuna mtendere wa Mulungu ndikuopa chilango chake. Ndithudi chilango cha Ambuye wako ndi chofuna kuopedwa

58Ndipo palibe mzinda umene Ife sitingauononge kapena kuulanga ndi chilango choopsa tsiku lachiweruzo lisanadze. Izi zidalembedwa m’Buku

59Ndipo palibe chimene chimatiletsa Ife kutumiza zizindikiro kupatula kuti anthu a mvula zakale sadazikhulupirire izo. Ndipo kwa anthu a Thamoud, Ife tidawapatsa ngamira yaikazi kukhala chizindikiro chooneka ndi maso komabe iwo adaichitira zoipa. Ndipo Ife sititumiza zizindikiro kupatula ndi cholinga chofuna kuchenjeza ndi kuwachititsa mantha

60Ndipo pamene tidakuuza kuti, “Ndithudi! Ambuye wako wawazungulira anthu. Ndipo Ife sitidapange masomphenya amene tidakuonetsa iwe koma kukhala mayeso kwa anthu chimodzimodzinso mtengo wotembereredwa umene watchulidwa m’Korani. Ife timawachenjeza ndi kuwachititsa mantha koma sizili kuwathandiza koma kuonjezera kusakhulupirira.”

61Ndipo pamene ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Onse adamugwadira iye kupatula Satana. Iye adayankha kuti, “Kodi ine ndimugwadire iye amene Inu mudamupanga kuchokera ku dothi?”

62Iye adati, “Mukumuona! Uyu ndiye amene mwamulemekeza kuposa ine ndipo ngati inu mundisunga ndi moyo mpaka patsiku louka kwa akufa, ine ndidzawasokoneza ana ake kupatula ochepa.”

63Mulungu adati, “Pita, ndipo aliyense wa iwo amene adzakutsatira, ndithudi, Gahena ndiyo idzakhala malipiro ake ndipo ndi malipiro okwana.”

64“Ndipo anyengerere amene ungawathe mwa iwo ndi mawu ako, ndipo menyana nawo ndi asirikali ako okwera akavalo ndi oyenda pansi, ndipo gawana nawo chuma ndi ana ndipo alonjeze.” Koma Satana sawalonjeza china chilichonse koma chinyengo

65“Ndithudi pa akapolo anga angwiro, iwe siudzakhala ndi mphamvu ina iliyonse pa iwo yowasokoneza. Ambuye wako ndi wokwana kukhala Mtetezi.”

66Ambuye wanu ndiye amene amayendetsa zombo pa nyanja kuti mufunefune zokoma zake. Ndithudi Iye ali wachisoni ndi inu

67Ndipo akakupezani mavuto pamene mulipanyanja, iwoamenemumawapembedzamowonjezera pa Iye amakuthawirani kupatula Iye yekha. Koma ngati Iye akupulumutsani kufika pa mtunda, mumatembenuka. Ndithudi, munthu ndi wamwano

68Kodi inu muli ndi chikhulupiriro chakuti Iye sangakumizeni m’dera lililonse la pamtunda kapena kuti sangakutumizireni mphepo yamkuntho? Pamenepo inu simudzapeza wina aliyense wokuthandizani

69Kapena inu mukukhulupirira kuti sangakubwezereninso m’nyanjamo kachiwiri ndi kukutumizirani mphepo yamkuntho, ndikukumizani chifukwa chakusakhulupirira kwanu ndipo kuti inu simudzapeza wokuthandizani polimbana ndi Ife

70Ndithudi Ife tawalemekeza ana a Adamu, ndipo Ife tawanyamula pamtunda ndi pa nyanja ndipo tawapatsa zinthu zabwino ndiponso tawalemekeza kuposa zina zimene talenga ndi ulemu wapadera

71Ndipo kumbukira tsiku limene tidzaitana mtundu uliwonse wa anthu pamodzi ndi Atsogoleri awo. Ndipo yemwe adzapatsidwa Buku lake ku dzanja lamanja iwo adzawerenga Bukulo mwa chisangalalo ndipo sadzaponderezedwa ngakhale ndi pang’onong’ono pomwe

72Koma iye amene ali wakhungu m’moyo uno adzakhalanso wakhungu m’moyo umene uli nkudza ndipo adzasochera kwambiri

73Ndithudi iwo adali pafupi kuti akusokoneze ku zimene takuvumbulutsira iwe kuti utinamizire zina ndipo zikadatero akadakupala ubwenzi

74Ngati Ife tikadapanda kulimbikitsa chikhulupiriro chako, padatsala pang’ono kuti uwatsatire

75Ndipo zikadatero Ife tikadakulawitsa chilango chachikulu m’moyo uno ndi chilango chachikulu m’moyo umene uli nkudza. Kotero siukadapeza wina aliyense wokuthandiza ku mkwiyo wathu

76Ndithudi adatsala pang’ono kukuchititsa mantha m’dziko ndi cholinga choti akuchotse m’menemo. Zikadatheka kutero iwo sakadakhala pambuyo pako, koma kwa kanthawi kochepa

77Umenewu ndiwo mwambo wa Atumwi amene tidatumiza iwe usanadze ndipo iwe siudzapeza kusintha kulikonse m’mwambo wathu

78Chita mapemphero kuyambira nthawi yopendekera dzuwakufikirausikundipowerenga Koranim’mapemphero a m’mbandakucha. Ndithudi kuwerenga Korani nthawi ya m’mbandakucha kumachitilidwa umboni

79Ndipo m’kati mwa usiku, pemphera ndi kuwerenga Korani ndi mapemphero oonjezera kwa iwe. Mwina Ambuye wako angadzakuike pamalo wotamandika

80Nena, “Ambuye ndilowetseni kulowa kwa bwino ndipo nditulutseni mwaubwino. Ndipo ndipatseni kuchokera kwa Inu mphamvu yondithandiza.”

81Nena, “Choonadi chadza ndipo bodza latha. Ndithudi bodza liyenera kutha.”

82Ndipo titumiza kuchokera m’Korani mankhwala ochiza ndiponso chisoni kwa onse okhulupirira, ndipo imaonjezera kwa anthu osakhulupirira chionongeko

83Ndipo tikam’patsa munthu zokoma zathu, iye amatembenuka ndi kuchita mwano ndipo amakhala kutali ndi njira yoyenera. Ndipo zikam’peza zoipa amakhala wotaya mtima kwambiri

84Nena, “Munthu aliyense amachita molingana ndi chikhalidwe chake koma Ambuye wanu amadziwa yemwe watsogozedwa bwino panjira yachilungamo.”

85IwoakukufunsazaMzimu.Ndiponena,“Ambuyewanga ndiye amene adziwa za iwo. Ndipo inu simudapatsidwe nzeru koma pang’ono pokha.”

86Ndithudi Ife tikadafuna, tikadakulanda chimene tavumbulutsa kwa iwe ndipo iwe siukadapeza wina aliyense wokuteteza kwa Ife m’malo mwako

87Kupatula chifundo chochokera kwa Ambuye wako, ndithudi ubwino wake pa iwe ndi waukulu zedi

88Nena, “Ngati anthu ndi majini akadagwirizana kubweretsa chofanana ndi Korani ino, iwo sakadabweretsa chofanana nayo ngakhale kuti iwo akadathandizana.”

89Ndithudi talongosola kwa anthu mu Korani ino chitsanzo chilichonse. Komabe anthu ambiri akana choonadi ndi kukhala osakhulupirira

90Iwo amati, “Ife sitidzakukhulupirira iwe mpaka pamene utatitumphutsira kasupe kuchokera pansi.”

91“Kapena utakhala ndi munda wa tende ndi mphesa ndipo m’kati mwake utumphutse mitsinjeyaikulu.”

92“Kapenaugwetsemtambopaifemonga momwe udatilonjezera kapena utibweretsere Mulungu pamodzi ndi angelo pamaso pathu.”

93“Kapena ukhale ndi nyumba yokongoletsedwa bwino kwambiri kapena ukwere kumwamba. Komabe ife sitidzakukhulupirira kukwera kwako mpaka pamene utatitsitsira ife Buku kuti tiziwerenga.” Nena, “Alemekezeke Ambuye wanga! Ndithudi ine sindine aliyense koma munthu amene watumizidwa ngati Mtumwi.”

94Ndipo palibe chimene chidawaletsa anthu kukhala okhulupirira pamene malangizo adadza kwa iwo koma mwano chifukwa iwo amati, “Kodi Mulungu watumiza munthu kukhala Mtumwi?”

95Nena, “Ngati angelo akadakhala pa dziko lapansi, namayenda mwamtendere, ndithudi, Ife tikadatumiza kwa iwo mngelo kuchoka kumwamba ngati Mtumwi.”

96Nena, “Mulungu ndi wokwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu. Ndithudi! Iye ndi wodziwa ndi woona zonse za akapolo ake.”

97Ndipo aliyense amene Mulungu wamutsogolera , atsogozedwa bwino koma iye amene Iye amusocheza wotere iwe siungamupezere mtetezi wina aliyense kupatula Iye yekha. Ndipo Ife tidzawasonkhanitsa onse pa tsiku la kuuka kwa akufa, akuyenda pa nkhope zawo, akhungu, abububu ndi agonthi, malo awo adzakhala Gahena ndipo pamene malawi ake azikazima tizidzawaonjezera moto

98Amenewo ndiwo malipiro awo chifukwa iwo sadakhulupirire mawu athu ndipo adati, “Pamene ife tidzasanduka mafupa ndi kufufutika, kodi tidzaukitsidwa kukhala chilengedwe chatsopano?”

99Kodi iwo saona kuti Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ali ndi mphamvu yolenga zofanana ndi iwo? Ndipo Iye adawaikira iwo nthawi yosakayikitsa. Komabe anthu ochimwa amakana choonadi ndikusankha kusakhulupirira

100Nena, “Ngati mukadakhala ndi nkhokwe za chifundo cha Ambuye wanga, ndithudi, inu mukanazibisa poopa kuti zingathe.” Ndithudi munthu ndi waumbombo

101Ndithudi Ife tidamupatsa Mose zizindikiro zisanu ndi zinayi zooneka. Afunse ana a Israyeli pamene iye adadza kwa iwo ndipo Farawo adati kwa iye, “Iwe Mose, ndithudi, ine ndili kukuganizira kuti ndiwe wolodzedwa.”

102Iye adati, “Ndithudi iwe uli kudziwa bwinobwino kuti zizindikiro izi sizinatumizidwe ndi wina koma Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ngati umboni wooneka ndi maso. Ndipo, ndithudi, ine ndiganiza kuti iwe, Farawo, ndiwe woonongeka.”

103Farawo anafunitsitsa kuti awapirikitse m’dziko. Koma Ife tidamumiza pamodzi ndi onse amene adali naye

104Ndipo pambuyo pake Ife tidati kwa ana a Israyeli, “Khalani m’dziko ndipo pamene lonjezo lomaliza lidzadza, Ife tidzakusonkhanitsani kukhala malo amodzi.”

105Ifetavumbulutsa Bukula Koranim’choonadindipondi m’choonadi latsika. Ndipo Ife takutumiza iwe osati wina kuti ukalalikire nkhani za bwino ndi kupereka chenjezo

106Ndi Buku la Korani limene tagawa m’zigawo kuti iwe uwerenge kwa anthu mwakanthawi. Ife talivumbulutsa pang’onopang’ono

107Nena, “Zili kwa inu kulikhulupirira kapena kusalikhulupirira. Ndithudi! Iwo amene adapatsidwa nzeru ilo lisadadze, likamawerengedwa kwa iwo, amagwetsa mphumi zawo pansi.”

108Ndipo iwo amati, “Ulemerero ndi wa Ambuye wathu! Ndithudi lonjezo la Ambuye wathu likwaniritsidwe.”

109Ndipo iwo amagwa pansi pa zipumi zawo, ali kulira ndipo limawaonjezera kudzichepetsa

110Nena, “Muitaneni Mulungu kapena Mwini chifundo chosatha, m’dzina lililonse limene mungamuitanire, chifukwa Iye ali ndi mayina abwino. Ndipo musanene mapemphero anu mokweza kapena motsitsa koma sankhani mawu a pakati ndi pakati.”

111Nena, “Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, amene sanabale mwana wamwamuna ndipo alibe mnzake womuthandiza mu Ufumu wake, ndipo Iye siwopanda mphamvu kuti angakhale ndi womuthandiza. Motero mulemekezeni Iye ndi ulemu woyenera Iye yekha.”

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath