104. Al-Humaza
1Tsoka kwa aliyense amene amajeda ndi kuononga mbiri ya anzake
2Amene amasonkhanitsa chuma chake ndi kumachiwerenga
3Iye amaganiza kuti chuma chake chidzamuchititsa iye kukhala ndi moyo wamuyaya
4Iyayi! Ndithudi iye adzaponyedwa ku moto woononga
5Kodi chidzakuuza kuti moto woononga ndi chiyani
6Ndi moto wa Mulungu umene Mwini wake anauyatsa
7Umene umafuka m’mitima ya anthu
8Ndithudi udzawatsekereza mbali iliyonse
9M’sanamila zoima
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath