Chisilamu
kubwerera

101. Al-Qaari'a

1Tsiku louka kwa akufa

2Kodi tsiku louka kwa akufa ndi chiyani

3Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze iwe kuti tsiku louka kwa akufa ndi chiani

4Ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati dzombe louluka paliponse

5Ndi mapiri adzakhala ngati fumbefumbe za ubweya

6Ndipo iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzakhala wolemera

7Adzakhala ndi moyo wa chimwemwe ndi chisangalalo

8Koma iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzapezeka wopepuka

9Mudzi wake udzakhala dzenje lamoto

10Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze zinthu zonsezi

11Ndi moto wa malawi osatha

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath