Chikhristu
kubwerera

AROMA 16

1Ine ndikupereka kwa inu mlongo wathu Febe, mtumiki wa mpingo wa ku Kenkreya.

2Ine ndikukupemphani kuti mumulandire mwa Ambuye mʼnjira yoyenera oyera mtima ndi kumupatsa thandizo lililonse limene akulifuna kuchokera kwa inu, pakuti iye wakhala thandizo lalikulu kwa anthu ambiri kuphatikiza ine.

3Perekani moni kwa Prisila ndi Akura, atumiki anzanga mwa Khristu Yesu.

4Iwo anapereka miyoyo yawo chifukwa cha ine. Osati ine ndekha komanso mipingo yonse ya a mitundu ina ikuyamika.

5Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo. Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.

6Perekani moni kwa Mariya, amene wakhala akukugwirirani ntchito kwambiri.

7Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.

8Perekani moni kwa Ampliato, amene ine ndimamukonda mwa Ambuye.

9Perekani moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu mwa Khristu ndi wokondedwa wanga Staku.

10Perekani moni kwa Apele, woyesedwa ndi wovomerezeka mwa Khristu. Perekani moni kwa a mʼbanja la Aristobulo.

11Perekani moni kwa Herodiona, mʼbale wanga. Perekani moni kwa a mʼbanja la Narkiso amene ali mwa Ambuye.

12Perekani moni kwa Trufena ndi Trufosa, amayi aja amene amagwira ntchito ya Ambuye molimbika. Perekani moni kwa mnzanga wokondedwa Persida, mayi winanso amene wagwira ntchito kwambiri mwa Ambuye.

13Perekani moni kwa Rufo, wosankhidwa mwa Ambuye, ndi amayi ake, amene akhala amayi anganso.

14Perekani moni kwa Asunkrito, Felego, Herima, Patroba, Herima ndi abale amene ali nawo pamodzi.

15Perekani moni kwa Filologo, Yuliya, Neriya ndi mlongo wake, ndi Olumpa ndi oyera mtima onse amene ali nawo pamodzi.

16Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona. Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.

17Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo.

18Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa.

19Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.

20Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu. Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.

21Timoteyo, mtumiki mnzanga, akupereka moni. Nawonso, Lusio, Yasoni ndi Sosipatro, abale anga akutero.

22Ine Tertio, amene ndalemba kalatayi, ndi kupereka moni mwa Ambuye.

23Gayo, amene chifukwa cha chisamaliro chake, ine ndi mpingo wonse kuno tikusangalala, akupereka moni. Erasto, amene ndi msungichuma wa mzinda wonse ndiponso mʼbale wathu Kwato, akupereka moni.

24Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.

25Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali,

26koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye,

27kwa Mulungu yekhayo wanzeru kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu! Ameni.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath