MASALIMO 9
1Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse; ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.
2Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu; Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.
3Adani anga amathawa, iwo amapunthwa ndi kuwonongedwa pamaso panu.
4Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga; Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.
5Mwadzudzula mitundu ya anthu ndipo mwawononga anthu oyipa; Inu mwafafaniza dzina lawo kwamuyaya.
6Chiwonongeko chosatha chagwera adani, mwafafaniza mizinda yawo; ngakhale chikumbutso chawo chawonongedwa.
7Yehova akulamulira kwamuyaya; wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira.
8Iye adzaweruza dziko mwachilungamo; adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.
9Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto.
10Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.
11Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni; lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
12Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira; Iye salekerera kulira kwa ozunzika.
13Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira! Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
14kuti ndilengeze za matamando anu pa zipata za ana aakazi a Ziyoni, kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
15Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba; mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
16Yehova amadziwika ndi chilungamo chake; oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo. Higayoni. Sela
17Oyipa amabwerera ku manda, mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.
18Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse, kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.
19Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane; mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
20Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova; mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba. Sela
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath