Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 92

1Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,

2Kulengeza chikondi chanu mmawa, ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,

3kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi ndi mayimbidwe abwino a zeze.

4Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova; Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.

5Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi!

6Munthu wopanda nzeru sadziwa, zitsiru sizizindikira,

7kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya.

8Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.

9Zoonadi adani anu Yehova, zoonadi adani anu adzawonongeka; onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.

10Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.

11Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane, makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.

12Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa, adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;

13odzalidwa mʼnyumba ya Yehova, adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.

14Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo, adzakhala anthete ndi obiriwira,

15kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama; Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath