MASALIMO 8
1Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba.
2Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda, Inu mwakhazikitsa mphamvu chifukwa cha adani anu, kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.
3Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake,
4munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira, ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
5Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
6Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu; munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
7nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi ndi nyama zakuthengo,
8mbalame zamlengalenga ndi nsomba zamʼnyanja zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.
9Inu Yehova, Ambuye athu, dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath