Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 85

1Yehova munakomera mtima dziko lanu; munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.

2Munakhululukira mphulupulu za anthu anu ndi kuphimba machimo awo onse. Sela

3Munayika pambali ukali wanu wonse ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.

4Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.

5Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?

6Kodi simudzatitsitsimutsanso, kuti anthu anu asangalale mwa Inu?

7Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova, ndipo tipatseni chipulumutso chanu.

8Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.

9Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye, kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.

10Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi; chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.

11Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi, ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.

12Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino, ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.

13Wolungama amapita patsogolo pake ndi kukonza njira za mapazi ake.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath