Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 83

1Inu Mulungu musakhale chete; musangoti phee, Mulungu musangoti duu.

2Onani adani anu akuchita chiwawa, amene amadana nanu autsa mitu yawo.

3Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu; Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.

4Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”

5Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:

6Matenti a Edomu ndi Aismaeli, Mowabu ndi Ahagiri,

7Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.

8Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo kupereka mphamvu kwa ana a Loti. Sela

9Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani, monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.

10Amene anawonongedwa ku Endori ndi kukhala ngati zinyalala.

11Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,

12amene anati, “Tiyeni tilande dziko la msipu la Mulungu.”

13Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga, ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.

14Monga moto umatentha nkhalango, kapena malawi a moto kuyatsa phiri,

15kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho, ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.

16Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.

17Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse; awonongeke mwa manyazi.

18Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath