MASALIMO 81
1Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu; Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!
2Yambani nyimbo, imbani tambolini imbani pangwe wolira bwino ndi zeze.
3Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;
4ili ndi lamulo kwa Israeli, langizo la Mulungu wa Yakobo.
5Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto, kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.
6Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo; Manja awo anamasulidwa mʼdengu.
7Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani, ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu; ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba. Sela
8“Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!
9Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu; musadzagwadire mulungu wina.
10Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto. Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.
11“Koma anthu anga sanandimvere; Israeli sanandigonjere.
12Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo kuti atsate zimene ankafuna.
13“Anthu anga akanangondimvera, Israeli akanatsatira njira zanga,
14nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!
15Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.
16Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri; ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath