MASALIMO 77
1Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo; ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
2Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye; usiku ndinatambasula manja mosalekeza ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.
3Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula; ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka. Sela
4Munagwira zikope zanga kuti ndisagone ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
5Ndinaganizira za masiku akale, zaka zamakedzana;
6Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku. Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,
7“Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya? Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
8Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu? Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
9Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima? Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”
10Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso: zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova; Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12Ndidzakumbukira ntchito zanu ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”
13Njira zanu Mulungu ndi zoyera. Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa; Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu, zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe. Sela
16Madzi anakuonani Mulungu, madzi anakuonani ndipo anachita mantha; nyanja yozama inakomoka.
17Mitambo inakhuthula madzi ake pansi, mu mlengalenga munamveka mabingu; mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu, mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19Njira yanu inadutsa pa nyanja, njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu, ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.
20Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath