Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 76

1Mulungu amadziwika mu Yuda; dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.

2Tenti yake ili mu Salemu, malo ake okhalamo mu Ziyoni.

3Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka, zishango ndi malupanga, zida zankhondo. Sela

4Wolemekezeka ndinu, wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.

5Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma, Iwowo amagona tulo tawo totsiriza; palibe mmodzi wamphamvu amene angatukule manja ake.

6Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo, kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.

7Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa. Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?

8Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo, ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,

9pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze, kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko. Sela

10Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.

11Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse; anthu onse omuzungulira abweretse mphatso kwa Iye amene ayenera kuopedwa.

12Iye amaswa mzimu wa olamulira; amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath