MASALIMO 75
1Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
2Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
3Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. Sela
4Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
5Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”
6Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu.
7Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
8Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.
9Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
10Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath