MASALIMO 6
1Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu.
2Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
3Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
4Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
5Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda?
6Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
7Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
8Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
9Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa.
10Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath