Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 62

1Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha; chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.

2Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.

3Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti? Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba, ngati mpanda wogwedezeka?

4Iwo akufunitsitsa kumugwetsa kuti achoke pa malo ake apamwamba. Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza. Ndi pakamwa pawo amadalitsa koma mʼmitima yawo amatemberera.

5Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga; chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.

6Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.

7Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu: Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.

8Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu; khuthulani mitima yanu kwa Iye, pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. Sela

9Anthu wamba ndi mpweya chabe; anthu apamwamba ndi bodza chabe; ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe; iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe

10Musadalire kulanda mwachinyengo kapena katundu wobedwa; ngakhale chuma chanu chichuluke, musayike mtima wanu pa icho.

11Mulungu wayankhula kamodzi, ine ndamvapo zinthu ziwiri; choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,

12komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika. Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu molingana ndi ntchito zake.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath