Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 59

1Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu; munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane.

2Landitseni kwa anthu ochita zoyipa ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi.

3Onani momwe iwo akundibisalira! Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane; osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.

4Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo. Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!

5Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse; musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.

6Iwo amabweranso madzulo akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyendayenda mu mzinda.

7Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo; iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo, ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?”

8Koma Inu Yehova, mumawaseka, mumayinyoza mitundu yonseyo.

9Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa.

10Mulungu wanga wachikondi. Mulungu adzapita patsogolo panga ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.

11Koma musawaphe, Inu Ambuye chishango chathu, kuopa kuti anthu anga angayiwale. Mwa mphamvu zanu, lolani kuti azingoyendayenda ndipo muwatsitse.

12Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo chifukwa cha mawu a milomo yawo, iwo akodwe mʼkunyada kwawo. Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula

13muwawononge mu ukali (wanu) muwawononge mpaka atheretu. Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi kuti Mulungu amalamulira Yakobo.

14Iwo amabweranso madzulo, akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyenda mu mzinda.

15Iwo amayendayenda kufuna chakudya ndipo amawuwa ngati sanakhute.

16Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu, mmawa ndidzayimba zachikondi chanu; pakuti ndinu linga langa, pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.

17Inu mphamvu yanga, ndiyimba matamando kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa, Mulungu wanga wachikondi.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath