Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 58

1Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama? Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?

2Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama, ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.

3Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera; kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.

4Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka, ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.

5Imene simva liwu la munthu wamatsenga, ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.

6Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu, Yehova khadzulani mano a mikango!

7Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.

8Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda; ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.

9Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku, kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.

10Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango, pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.

11Ndipo anthu adzanena kuti, “Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho; zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath