MASALIMO 53
1Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.
2Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano pa ana a anthu kuti aone ngati alipo wina wanzeru, wofunafuna Mulungu.
3Aliyense wabwerera, iwo onse pamodzi akhala oyipa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino, ngakhale mmodzi.
4Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi; anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi, ndipo sapemphera kwa Mulungu?
5Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.
6Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni! Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake, lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath