Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 52

1Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu? Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse, iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?

2Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena; lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nʼkunyenga.

3Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi. Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona. Sela

4Umakonda mawu onse opweteka, iwe lilime lachinyengo!

5Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya: iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako; iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.

6Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha; adzamuseka nʼkumanena kuti,

7“Pano tsopano pali munthu amene sanayese Mulungu linga lake, koma anakhulupirira chuma chake chambiri nalimbika kuchita zoyipa!”

8Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu; ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu kwa nthawi za nthawi.

9Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita; chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath