Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 4

1Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

2Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? Sela.

3Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika; Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.

4Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. Sela

5Perekani nsembe zolungama ndipo dalirani Yehova.

6Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?” Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.

7Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.

8Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath