Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 49

1Imvani izi anthu a mitundu yonse; mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,

2anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika, olemera pamodzinso ndi osauka:

3Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru; mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.

4Ndidzatchera khutu langa ku mwambo, ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.

5Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika, pamene achinyengo oyipa andizungulira.

6Iwo amene adalira kulemera kwawo ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?

7Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.

8Dipo la moyo ndi la mtengowapatali, palibe malipiro amene angakwanire,

9kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya ndi kusapita ku manda.

10Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.

11Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya, malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo, ngakhale anatchula malo mayina awo.

12Ngakhale munthu akhale wachuma chotani, adzafa ngati nyama.

13Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha, ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. Sela

14Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda, ndipo imfa idzawadya. Olungama adzawalamulira mmawa; matupi awo adzavunda mʼmanda, kutali ndi nyumba zawo zaufumu.

15Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda; ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.

16Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;

17Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira, ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.

18Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,

19iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake, amene sadzaonanso kuwala.

20Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru adzafa ngati nyama yakuthengo.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath