Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 46

1Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.

2Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,

3ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu, ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

4Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu, malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.

5Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa; Mulungu adzawuthandiza mmawa.

6Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa; Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

7Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

8Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova, chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.

9Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo; amatentha zishango ndi moto.

10Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”

11Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath