MASALIMO 45
1Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu; lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
2Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika, popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
3Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu; mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.
4Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo; dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
5Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu, mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.
6Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi; ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
7Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa; choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
8Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya; kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
9Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka; ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
10Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu; iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako; mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso, amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake, chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu; anamwali okhala naye akumutsatira ndipo abweretsedwa kwa inu.
15Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo; akulowa mʼnyumba yaufumu.
16Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako; udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse; choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath