MASALIMO 44
1Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.
2Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena ndi kudzala makolo athu; Inu munakantha mitundu ya anthu, koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
3Sanalande dziko ndi lupanga lawo, si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso, koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu, pakuti munawakonda.
4Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
5Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu; kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
6Sindidalira uta wanga, lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
7koma Inu mumatigonjetsera adani athu, mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
8Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse, ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.
9Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa; Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
10Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
11Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
12Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika, osapindulapo kanthu pa malondawo.
13Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina, chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
14Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina; anthu amapukusa mitu yawo akationa.
15Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
16chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe, chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.
17Zonsezi zinatichitikira ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
18Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo; mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
19Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.
20Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
21kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi, pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
22Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse, tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.
23Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona! Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
24Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu, ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?
25Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi; matupi athu amatirira pa dothi.
26Imirirani ndi kutithandiza, tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath