MASALIMO 42
1Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi, kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
2Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo. Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
3Misozi yanga yakhala chakudya changa usana ndi usiku, pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?”
4Zinthu izi ndimazikumbukira pamene ndikukhuthula moyo wanga: momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu, kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko pakati pa anthu a pa chikondwerero.
5Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Yembekezera Mulungu, pakuti ndidzamulambirabe, Mpulumutsi wanga ndi
6Mulungu wanga. Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga kotero ndidzakumbukira Inu kuchokera ku dziko la Yorodani, ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
7Madzi akuya akuyitana madzi akuya mu mkokomo wa mathithi anu; mafunde anu onse obwera mwamphamvu andimiza.
8Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake, nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane; pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.
9Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa, “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?”
10Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo pamene adani anga akundinyoza, tsiku lonse akunena kuti, “Mulungu wako ali kuti?”
11Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath