MASALIMO 3
1Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira!
2Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela
3Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
4Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela
5Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
6Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
7Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa.
8Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. Sela
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath