MASALIMO 34
1Ndidzayamika Yehova nthawi zonse; matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.
2Moyo wanga udzanyadira Yehova; anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.
3Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine; tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.
4Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse.
5Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira; nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.
6Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.
7Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa.
8Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino; wodala munthu amene amathawira kwa Iye.
9Wopani Yehova inu oyera mtima ake, pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.
10Mikango itha kulefuka ndi kumva njala koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.
11Bwerani ana anga, mundimvere; ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.
12Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,
13asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.
14Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; funafuna mtendere ndi kuwulondola.
15Maso a Yehova ali pa olungama ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;
16nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa, kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.
17Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.
18Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.
19Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri, Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,
20Iye amateteza mafupa ake onse, palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.
21Choyipa chidzapha anthu oyipa; adani a olungama adzapezeka olakwa.
22Yehova amawombola atumiki ake; aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath