Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 32

1Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa.

2Ngodala munthu amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.

3Pamene ndinali chete, mafupa anga anakalamba chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.

4Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu linandipsinja; mphamvu zanga zinatha monga nthawi yotentha yachilimwe. Sela

5Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” Sela

6Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo pomwe mukupezeka; ndithu pamene madzi amphamvu auka, sadzamupeza.

7Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. Sela

8Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.

9Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.

10Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa koma chikondi chosatha cha Yehova chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.

11Kondwerani mwa Yehova inu olungama; imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath