MASALIMO 30
1Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
2Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.
3Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.
4Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera.
5Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.
6Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.”
7Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima.
8Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
9“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.”
11Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath