MASALIMO 28
1Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa; musakhale osamva kwa ine. Pakuti mukapitirira kukhala chete, ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
2Imvani kupempha chifundo kwanga pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize, pomwe ndikukweza manja anga kuloza ku malo anu oyeretsetsa.
3Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa, pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa, amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
4Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo ndi ntchito zawo zoyipa; abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
5Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova, ndi zimene manja ake anazichita, Iye adzawakhadzula ndipo sadzawathandizanso.
6Matamando apite kwa Yehova, popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
7Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
8Yehova ndi mphamvu ya anthu ake, linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
9Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu; mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath