MASALIMO 26
1Weruzeni Inu Yehova pakuti ndakhala moyo wosalakwa. Ndadalira Yehova popanda kugwedezeka.
2Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni, santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
3pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse, ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
4Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo, kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
5Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
6Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
7kulengeza mofuwula za matamando anu ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
8Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo, malo amene ulemerero wanu umapezekako.
9Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa, moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
10amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa, dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
11Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa; mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.
12Ndayima pa malo wopanda zovuta ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath