MASALIMO 23
1Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.
4Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
5Mumandikonzera chakudya adani anga akuona. Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chimasefukira.
6Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova kwamuyaya.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath