MASALIMO 20
1Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
2Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika; akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
3Iye akumbukire nsembe zako zonse ndipo alandire nsembe zako zopsereza. Sela
4Akupatse chokhumba cha mtima wako ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
5Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
6Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
7Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
8Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa, koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.
9Inu Yehova, pulumutsani mfumu! Tiyankheni pamene tikuyitanani!
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath