MASALIMO 17
1Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo; mverani kulira kwanga. Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
2Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu; maso anu aone chimene ndi cholungama.
3Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku, ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu; Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
4Kunena za ntchito za anthu, monga mwa mawu a pakamwa panu, Ine ndadzisunga ndekha posatsata njira zachiwawa.
5Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu; mapazi anga sanaterereke.
6Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha; tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
7Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu, Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
8Mundisunge ine ngati mwanadiso; mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
9kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine, kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.
10Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo, ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
11Andisaka, tsopano andizungulira ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
12Iwo ali ngati mkango wofuna nyama; ngati mkango waukulu wokhala mobisala.
13Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi; landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
14Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere, kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno. Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu; ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri, ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
15Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu; pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.
gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
WEBREATH · 11:11
«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath