Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 16

1Ndisungeni Inu Mulungu, pakuti ine ndimathawira kwa Inu.

2Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga; popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”

3Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko, amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.

4Anthu amene amathamangira kwa milungu ina mavuto awo adzachulukadi. Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.

5Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa; mwateteza kolimba gawo langa.

6Malire a malo anga akhala pabwino; ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.

7Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.

8Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

9Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera; thupi langanso lidzakhala pabwino,

10chifukwa Inu simudzandisiya ku manda, simudzalola kuti woyera wanu avunde.

11Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath