Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 15

1Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?

2Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,

3ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,

4amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka,

5amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezi sadzagwedezeka konse.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath