Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 150

1Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.

2Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu; mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.

3Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.

4Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina, mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.

5Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga, mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.

6Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath