Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 148

1Tamandani Yehova. Tamandani Yehova, inu a kumwamba, mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.

2Mutamandeni, inu angelo ake onse, mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.

3Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.

4Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.

5Zonse zitamande dzina la Yehova pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.

6Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi; analamula ndipo sizidzatha.

7Tamandani Yehova pa dziko lapansi, inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,

8inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo, mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,

9inu mapiri ndi zitunda zonse, inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,

10inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse, inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.

11Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.

12Inu anyamata ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe.

13Onsewo atamande dzina la Yehova pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka; ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.

14Iye wakwezera nyanga anthu ake, matamando a anthu ake onse oyera mtima, Aisraeli, anthu a pamtima pake. Tamandani Yehova.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath