Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 146

1Tamandani Yehova. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

2Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

3Musamadalire mafumu, anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.

4Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi; zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.

5Wodala ndi amene thandizo lake ndi Mulungu wa Yakobo.

6Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo; Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.

7Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala. Yehova amamasula amʼndende,

8Yehova amatsekula maso anthu osaona, Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi, Yehova amakonda anthu olungama.

9Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

10Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse. Tamandani Yehova.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath