Chikhristu
kubwerera

MASALIMO 145

1Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga; ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.

2Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

3Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse; ukulu wake palibe angawumvetsetse.

4Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina; Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.

5Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

6Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri, ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.

7Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu, ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.

8Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

9Yehova ndi wabwino kwa onse; amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.

10Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova; oyera mtima adzakulemekezani.

11Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu ndi kuyankhula za mphamvu yanu,

12kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.

13Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.

14Yehova amagwiriziza onse amene akugwa ndipo amakweza onse otsitsidwa.

15Maso a onse amayangʼana kwa Inu, ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.

16Mumatsekula dzanja lanu ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.

17Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse, ndi wokonda zonse zimene anazipanga.

18Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.

19Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa; amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.

20Yehova amayangʼana onse amene amamukonda koma adzawononga anthu onse oyipa.

21Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova. Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera ku nthawi za nthawi.

gwero: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

WEBREATH · 11:11

«He himself gives everyone life and breath and everything else» — Acts 17:25

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath